Boma kudzera ku unduna wa zamaphunziro lalamula kuti ophunzira onse a fomu folo abweleleso ku sukulu pa 28 December poomwe akuyembezeka kukalembaso mayeso mu January chaka chamawa ndipo lati onse sakuyeneraso kulipira ndalama iliyonse.
Izi ndimalingana ndichikalata chomwe unduna wazamaphunziro watulutsa dzulo chomwe chasainidwa ndi mlembi wamkulu mu undunawu a Chikondano Mussa.
Pa 4 November chaka chino, boma kudzera kuunduna wa maphunziro linalengeza zakuyimitsidwa kwa mayeso a MSCE omwe anali mkati kulembedwa ati kaamba koti mayesowa anaoneredwa kwambiri.
Chiganizo choimitsa mayesowa chinabwera pomwe akuluakulu a bungwe loyendetsa mayeso la Maneb anapeza kuti pafupifupi pepala lililonse la mayesowa, ophunzira ochuluka amakhala ataliona kale tsiku loti lilembedwe lisanafike.
Apa bungwe la Maneb linaika mwezi wa March kuti ndiomwe mayesowa adzalembedweso koma mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera anakana ponena kuti March kwatalika ndipo m’malo mwake analamula kuti mayesowa alembedweso mu January.
Ndipo potsatira mawu a Chakwera, unduna wamaphunziro walengeza kuti mayesowa alembedwaso mu January chaka chamawa ndipo walamula kuti ophunzira a folom folo masukulu aboma kapena sukulu zoima pazokha, onse apiteso ku masukulu awo pa 28 December.
Malingana ndi chikalata chomwe undunawu watulutsachi, ophunzira wina aliyese sakuyenera kukapelekaso ndalama ina iliyose ya fizi kapena ya mayeso ati ponena kuti chilichose chofuna ndalama, lipeleka ndi boma.
Apa boma lati likudziwa kuti ndalama ya fizi komaso yamayeso yomwe ophunzira anapeleka, inali isanathe kugwira ntchito yake ndipo latsindika kuti sukulu ili yonse isauze ophunzira kuti apeleke ndalama inailiyonse.
Boma lalamulaso kuti ophunzira onse omwe asankhidwe kukayamba form one, adzayenera kukayamba sukulu pa 1 February zomwe ati ndi kaamba kofuna kuchepetsa kuthithikana pomwe mayeso a MSCE akhale akulembedwa.
Ngakhale zili choncho, unduna wamaphunzirowu walengezaso kuti ophunzira a Forms 2, form 3, komaso omwe akakhale akuyamba form 4 azatsekulira sukulu pa 5 January motsatira calendala ya maphunziro ya 2021.