CAMA yaikira kumbuyo ganizo lokweza mitengo ya mafuta

Bungwe loyang’anira ufulu wa anthu ogula m’dziko muno la Consumers Association of Malawi, (CAMA) laikira kumbuyo ganizo laboma lofuna kukweza mitengo ya mafuta a galimoto.

Izi zikutsatira mphekesera yomwe yakhala ikuveka posachedwa yoti boma litha kukweza mitengo ya mafuta mwezi uno zomwe zikupeleka chiopsezo choti mitengo yazinthu zina ithaso kukwera.

Potsatira mphekeserayi, nduna yowona za mphamvu ndi mafuta a Newton Kambala sabata latha anatsimikizira imodzi mwa mawailesi m’dziko muno kuti boma lilidi ndi ganizo lokweza mitengo ya mafutayi.

Poyankhulapo pankhaniyi, mtsogoleri wa bungwe la CAMA a John Kapito ati iwo sakuona vuto lililonse ndiganizo lofuna kukweza mitengo yamafutayi.

A Kapito ati maiko ambiri omwe anaimitsa ntchito zawo zamalonda kaamba ka mlili wa COVID-19, ayambiraso ntchitozo zomwe zikupereka chithuzithuzi choti zinthu ziyambiraso kuyenda bwino ngati kale.

Iwo anatiso zomwe boma linalamula kuti masukulu komaso mabwalo a ndege atsekulidwe mwezi uno ndichisonyezo choti zinthu zambiri zikubweleraso kuchitika ngati ndipo anati kukweza mitengo ya mafutayi sikuti zingapangitse kuti mitengo yazinthu zina ikwere.

“Kwacha yathu ikakhala ndi mphamvu zimapangitsaso kuti mafuta aja kuno azigulidwa pa mitengo yotsika. Pakatipa mitengo yazinthu zambiri inatsika kaamba ka mlili wa COVID-19 koma pano tamva tonse kuti maiko ambiri ndege zikuyambaso kuyenda zomwe zipangitse kuti mitengo yazinthu zinaso ikwere.

“Pakatipa panalibe zinthu zenizeni zogwiritsa ntchito mafuta zomwe zinapangitsa kuti mitengo ija itsitsidwe ndipo ndikuona kuti mitengoyo ngakhale atati akweze pano palibe anthu omwe aziyankhula,” watero Kapito.

Pakadali pano mafuta a mtundu wa petulo akugulitsidwa pa mtengo wa K690.50 pomwe dizilo alipa K664.80 ndipo mafuta amtundu wa parafini alipa mtengo wa K441.70. Mitengoyi inapangidwa mu May chaka Chino.

Advertisement