Bambo aphedwa, adulidwa ziwalo zobisika

Advertisement

Bambo Reuben Mpika a zaka 48 ochokela m’mudzi mwa Mkamile mfumu yaikulu Chilooko Ku Ntchisi aphedwa ndi anthu achifwamba omwe adulaso ziwalo zobisika za bamboyo.

Omwe atidziwitsa za nkhaniyi, anena kuti bambo Reuben anapita kokumwa mowa pa 6 March sabata latha pa malo oyandikana ndi pomwe achitidwa chiwembucho ndipo sanabwelele kwao.

Mam’mawa wa tsiku loweluka, bambo Reuben anapezeka m’mbali mwa ntsinje wa Ntuwanjovu Ku Ntchisi komweko.

M’neneli wa a polisi Ku Ntchisi a Mwakayoka Kaponda avomeleza za nkhaniyi.

“Titamvesedwa za nkhaniyi, ife a polisi tinatengela bambo Reuben ku chipatala. Uko madotolo ananena kuti bambo Reuben anamwalila kamba kotaya magazi ochuluka atadulidwa maliseche,” anatelo a Kaponda.

A Kaponda ananenanso kuti a polisi Ku Ntchisi ali pakalikiliki kufufufuza yemwe wapanga chipongwe bamboyi ndipo akapezeka akayankha mulandu okupha.

Advertisement