Boma kudzera mu unduna wa m’maboma ang’ono ndi chitukuko lati ndilokhutira ndim’mene ikuyendera ndondomeko yopeleka mphamvu ku anthu m’dziko muno.
Izi ndi malinga ndim’modzi mwa akuluakulu a ku undunawu a Sphiwe Mauwa omwe amayankhula lachinayi ku Mponela m’boma la Dowa pakutha pa maphunziro a olemba nkhani pa momwe angathandizile kupititsa patsogolo ndondomeko ya mphamvu ku anthu.
A Mauwa anati atolankhani ali ndi udindo waukulu pakayendetsedwe kaboma ndipo anati ndi chifukwa chake anawaitanitsa kuti awaphunzitse momwe angalembere nkhani komaso kupanga ma pologalamu a ndondomeko ya mphamvu ku anthu.
Malingana ndi a Mauwa, ndondomeko ya mphamvu ku anthu, ikuyenda bwino ngakhale kuti pali madera ena omwe akutsalirabe koma ati madera omwe akutsalawo ayesetsa kuti atheke pomatha chaka chino.
Iwo anati kuyambila mchaka chomwe boma linakhazikitsa ndondomekoyi, anthu akumudzi ayamba kupatsidwa maudindo ndi mphamvu pakayendetsedwe kazinthu zosiyana siyana mmaboma awo.
“Ife a unduna wa maboma ang’ono ndichitukuko tinaganiza zoitanitsa atolankhani ndicholinga choti atithandize kupeleka uthenga okhudza ndondomeko ya mphamvu ku anthu. Chiyambileni ndondomekoyi pachitika zinthu zambiri, zina zabwino zina zolakwika.
“Pakadali pano takwanitsa kuphunzitsa makhonsolo kuzidalira paokha komaso tsopano anthu omwe anali ku boma tsopano akugwira ntchito mmakhonsolo. Panopa chimene chatsala ndichoti katundu achoke ku boma apite kukhonsolo ndipo tikamaliza izi tikhala kuti tayesetsa pankhani yopeleka mphamvu ku anthu,” anatero Mauwa.
Apa a Mauwa anaonjezera kuti kudzeraso mu ndondomeko ya mphamvu ku anthuyi, anthu a m’mamidzi akumapasidwa mphamvu zoitanitsa chitukuko chomwe akuchifuna kudzera kwa ma khansala ammadera awo.
Boma kudzera ku unduna wa maboma ang’ono ndichitukuko inakhazikitsa ndondomeko ya mphamvu ku anthu mumchaka cha 1998 ndicholinga chofuna kupereka mphamvu kwa anthu akumudzi pakayendetsedwe ka zitukuko zosiyana siyana.
Ndondomekoyi ikuyendetsedwa ndi unduna wa maboma ang’ono ndithandizo lochokera ku mabungwe a USAID komaso UKAID kudzela ku ndondomeko ya Local Government Accountability Performance (LGAP)