Boma likweza mtengo wa pasipoti

Advertisement

Boma kudzera ku nthambi lowona za anthu olowa ndikutuluka m’dziko muno la Immigration latsimikiza kuti posachedwapa likweza mitengo ya ziphaso zoyendera.

Poyankhula ndi nyuzipepala ino mneneri wa bungweli a Joseph Chauwa anati mphekeserayi ndiyoona koma akudikira kuti nkhaniyi akaisiye kunyumba yamalamulo kuti aphungu akaikambilane ndipo ngati aphunguwa angavomereze, chiphasochi chikwera.

A Chauwa anati chatsitsa dzaye ndikaamba koti ndalama yadziko lino pakatipa yagwa mphavu zomwe zapangitsa kuti mitengo yazinthu ikwere komaso ati papita nthawi yaitali iwo chikwezereni mtengo wachiphasochi mumchaka cha 2009.

Mneneriyu wati boma likumasakaza ndalama zochuluka anthu akamapangitsa ziphaso zawo ponena kuti chiphaso chilichose boma limaikapo ndalama yosachepela K80,000 zomwe ati ndizokwera kwambiri.

Mkuluyu wati pakadali pano ngakhale sizinadziwike kuti mtengowu ukwera motani komaso ukwera liti, koma boma likufuna kuti aliyese azizipangira yekha chiphaso chake pofuna kuchepetsa ndalama zomwe boma likumaononga.

Izi zikutanthauza kuti boma siliziikaso ndalama iliyose munthu akamapangitsa chiphaso chake zomwe zingapangitse kuti mtengo wachiphasowu ukwere ndi ndalama yochuluka kwambiri.

“Ndizoonadi, ife tinafusidwa kuti tiunikeso mitengo yazinthu zimene timapeleka kwa anthu kuphatikizapo passport. Chachikulu chomwe chapangitsa mchakuti mtengo wapanowu ndiwotsika kwambiri poyelekeza ndi ndalama zomwe zimalowa kuti pasipoti iliyonse ituluke bwino bwino.

“Pamtengo wapanopawu boma likumalowetsa ndalama pafupifupi K80,000 pa passport imodzi nde chomwe tikufuna kuchita ndichoti munthu azingopeleka mtengo wa zonse zomwe zimalowa pa pasipoti zomwe zikutanthauza kuti zikatero boma siliziikaso ndalama iliyonse munthu akamapangigsa chiphaso chake,” anatero Chauwa.

Mkuluyu anati pakadali pano bungwe lawo likuunika bwino bwino zankhaniyi ndipo akamaliza kuunikaku ayitengera nkhaniyi Ku nyumba yamalamulo kuti aphungu akavomeleze kapena kutsutsa zakukwezaku.

Pakadali pano, mphekesera zosatsimikizika zikusonyeza kuti ngati aphungu anyumba ya malamulo angavomereze kukweza mtengowu, chiphaso chotchipa chichoka pa mtengo wa K48,500 ndikufika pa K80,000.