Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino yemweso ndi mtsogoleri wa chipani cha UTM a Saulos Chilima waulura kuti chipani cholamula cha DPP chikusolola ndalama ku ma kampani awiri a boma.
Poyankhula Ku khwimbi la anthu omwe anasonkhana Ku Neno pa msonkhano wake okopa anthu lachitatu lapitali, Chilima anati chipani cha DPP chikumatenga ndalama ku kampani ya Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) komaso Malawi Revenue Authority (MRA).
A Chilima anati bungwe lotolera misonkho la MRA likumapereka ma khadi (card) a mafuta a galimoti kwa akuluakulu a chipani cholamula maka ochokera mchigawo chapakati komaso chigawo chakummwera.
Iwo anatsindika za nkhaniyi ndipo anafotokoza kuti ali ndi umboni kuti chipani cha DPP chikusolola ndalama zankhaninkhani ku mabungwe awiriwa zomwe anati ndizokhumudwitsa kamba koti ndalama zikutengedwazi zimayenera kugwira ntchito zina za chitukuko.
“Ndili ndi umboni onse ndipo ndikudziwa malo omwe anthuwa akumathira mafuta mugalimoto zawo Ku Lilongwe ndiku Blantyre komaso ndili ndi manambala amakhadi omwe akugwiritsa ntchito. Ndili ndiumboni ndithudi koma sindinena chifukwa olo ndinene palibe chomwe angachite.
“Ngati akuona ngati ndikunama achite kafukufuku komaso atilore ifeso tichite kafukufuku momwe ma kampani awiriwa akugwilitsira ntchito ndalama zake.
“Khalidwe ili lomaononga ndalama za boma litheretu,” anatero Chilima.
Izi zikutsatira zomwe boma lanena posachedwapa zoti ngati Chilima angapitilize kumaliloza chala liulura zonse zoipa komaso zinsinsi zomwe mkuluyu wakhala akuchita.
Koma wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu anati iye sakuopa kena kalikose ndipo ananenetsa kuti boma silingamuopyseze mwanjira iliyonse ndipo boma lili lomasuka kuulura zinsinsi zake zonse.