Satana walephera – Chaponda

George Chaponda

Anthu amene safunila a George Chaponda zabwino, anthu amene asanadye pemphero lawo limakhala lopempha Mulungu kuti mwina angozimitsa a Chaponda, ati ndi amene ankapanga upo ofuna kugwetsa a Chaponda koma alephera.

Nduna yakale ya zaulimi a George Chaponda imene dzulo yapezeka kuti ilibe mlandu oti iyankhe pa nkhani yoganizilidwa kuti amafuna kuchita katangale yati chigamulo cha Khoti dzulo changosonyeza kuti iye amanena zoona zoti ndi osalakwa.

George Chaponda
Chaponda alibe mlandu

A Chaponda amene ndi wachiwiri kwa President wa chipani cholamula cha DPP ku chigawo cha kummwela anaimitsidwa pa unduna zitamveka zoti anachita kusalungama pa nkhani ya chimanga. Iwo amakakamila kuti anthu osawafunila zabwino awasemela chinyau.

Polankhulapo patapelekedwa chigamulo, a Chaponda athokoza a Peter Mutharika kamba kosawachotsa mu chipani ngakhale kuti anthu ochuluka anafuna kuwachotsa.

“Choyamba, chigamulochi ndi umboni oti anthu amandida basi. Analibe nane nkhani,” anatelo a Chaponda kenako anapitiliza:

“Koma ndithokozenso a president Peter Mutharika kuti sanamvele zokamba za anthu ndipo anandisiyila udindo waukulu ku chipani.”

 

Advertisement

2 Comments

  1. Aaaa koma ndalam zakunja zipeka bwNji ndi chaponda? Koma chigamulo sichinalongosoke baba. Kalipo kalipo.

Comments are closed.