Bushiri, Mboro khethekhethe tsopano

Advertisement
Bushiri

Ati asiya zokokanakokana. Tsopano ndi amodzi ndipo agwilila ntchito limodzi. Ndipo apo mwaona Bushiri, yembekezani kuona Mboro.

Mneneri Shepherd Bushiri amene ali ku South Africa ati wagwilizana ndi M’busa wa ku South Africa komweko wa dzina lachilendo Mboro.

Bushiri
Bushiri agwilizana ndi M’busa Mboro.

Awiliwa ati akhala akukulilana mtima ndipo mpaka anafika mothilana kachipongwe mwachinsinsi.

Koma ati ataona kuti gwilugwilu wawo sakuphula kanthu, Bushiri anakanyonyomala kwa Mboro kukapempha kuti agwile ntchito limodzi. Ndipo Mboro anavomela.

Mboro anatchuka mmbuyomu ndi nkhani yoti anapita kumwamba, koma malipoti a nyuzipepa ati nkhani imeneyi inali yabodza ndipo analemba ndi anyamata a Bushiri.

Olankhulila a Bushiri, a Ephraim Nyondo auza olemba nkhani kuti kubwela pamodzi kwa a Bushiri ndi a Mboro ndi nkhani yabwino.