Bushiri, Mboro khethekhethe tsopano

Advertisement
Bushiri

Ati asiya zokokanakokana. Tsopano ndi amodzi ndipo agwilila ntchito limodzi. Ndipo apo mwaona Bushiri, yembekezani kuona Mboro.

Mneneri Shepherd Bushiri amene ali ku South Africa ati wagwilizana ndi M’busa wa ku South Africa komweko wa dzina lachilendo Mboro.

Bushiri
Bushiri agwilizana ndi M’busa Mboro.

Awiliwa ati akhala akukulilana mtima ndipo mpaka anafika mothilana kachipongwe mwachinsinsi.

Koma ati ataona kuti gwilugwilu wawo sakuphula kanthu, Bushiri anakanyonyomala kwa Mboro kukapempha kuti agwile ntchito limodzi. Ndipo Mboro anavomela.

Mboro anatchuka mmbuyomu ndi nkhani yoti anapita kumwamba, koma malipoti a nyuzipepa ati nkhani imeneyi inali yabodza ndipo analemba ndi anyamata a Bushiri.

Olankhulila a Bushiri, a Ephraim Nyondo auza olemba nkhani kuti kubwela pamodzi kwa a Bushiri ndi a Mboro ndi nkhani yabwino.

Advertisement

4 Comments

  1. Iwe Kondwani udziona Kaye nkhani ya kalembedwe ka mau usanatsindikize nkhani wamva eti. Mumatichitsa manyazi. Kodi kusukulu komwe udapitako dictation kudalibe? Poyenera r iwe ukuikapo l.

    Bushiri and his partner are conmen so don’t be surprised because birds of the same feathers flock together. Woe to those who believes that these guys are true messengers of God because they’re believing in faulse Prophets. These guys shall drink the “THE WINE OF THE WRATH OF GOD WITHOUT MIXTURE” because they’re leading people astray from the kingdom of God. The most pity thing is that their followers are spiritually maiopic so the fail to see things from a nook. MAY GOD HAVE MESSY ON US BECAUSE TIME IS OVER BUT WE’RE STILL DELUDING OURSELVES THAT WE’LL GET SAVED EVEN IF WE’RE FOLLOWING A DEVIL’S ADVOCATE AND AN ADVOCATE OF THE DEVIL. But God is merciful and HE is still calling “get out of there yes my people.”

  2. Tiona kt ubale umenewu ufika mpaka lit……..kkkkk km maina enawa

Comments are closed.