2019, tikuyambapo ntchito yokonza zonse waononga Mutharika – atelo a Chakwera

Advertisement
Lazarus Chakwera

Ati a Mutharika ndi chipani chawo cha Democratic Progressive (DPP) agwilira dziko lino. Aliveka manyazi. Kuliyamwa kalikonse ndi kulisiya mbu. Lokhuta ndi umphawi.

Koma a Malawi musadandaule, chifukwa ati a Chakwera ndi chipani chawo cha Kongeresi akonza zonsezi akalowa m’boma mu chipani cha 2019.

Lazarus Chakwera
Chakwera: a Mutharika aononga dziko lino.

Mtsogoleri wa chipani chotsutsa a Lazarus Chakwera wati chipani cha DPP chikutuluka m’boma ndipo alowemo ndi iwo a Kongeresi mu chaka cha 2019.

Poyankhula pa mwambo wa kantoletole omwe unachitika mu mzinda wa Blantyre, a Chakwera amene akuyembekezeka kupikisana kwambiri ndi a Mutharika mu chaka cha 2019 ananena kuti a Malawi ambiri ndi okhumudwa ndi utsogoleri wa a Mutharika ndi chipani chawo cha DPP.

Iwo anati a Mutharika aononga dziko lino ndipo pofika 2019, a Malawi samvela ndi komwe nthano zimene a Mutharika angabwele nazo pa kampeni.

“Azanena kuti akufuna achite chani chimene chingasunthe a Malawi?” anadabwa a Chakwera.

“Mu zaka zinayi izi alephera kuchita kanthu, kuwaonjezela zaka zina kodi iwowa achitapo chani?” anaonjezelapo a Chakwera.

Kwabwela nyonga ku Kongeresi kuyambila pamene chipanichi chidabweletsa a Sidik Mia amene dzulo anakhala chifupi ndi a Chakwera.