2019, tikuyambapo ntchito yokonza zonse waononga Mutharika – atelo a Chakwera

Advertisement
Lazarus Chakwera

Ati a Mutharika ndi chipani chawo cha Democratic Progressive (DPP) agwilira dziko lino. Aliveka manyazi. Kuliyamwa kalikonse ndi kulisiya mbu. Lokhuta ndi umphawi.

Koma a Malawi musadandaule, chifukwa ati a Chakwera ndi chipani chawo cha Kongeresi akonza zonsezi akalowa m’boma mu chipani cha 2019.

Lazarus Chakwera
Chakwera: a Mutharika aononga dziko lino.

Mtsogoleri wa chipani chotsutsa a Lazarus Chakwera wati chipani cha DPP chikutuluka m’boma ndipo alowemo ndi iwo a Kongeresi mu chaka cha 2019.

Poyankhula pa mwambo wa kantoletole omwe unachitika mu mzinda wa Blantyre, a Chakwera amene akuyembekezeka kupikisana kwambiri ndi a Mutharika mu chaka cha 2019 ananena kuti a Malawi ambiri ndi okhumudwa ndi utsogoleri wa a Mutharika ndi chipani chawo cha DPP.

Iwo anati a Mutharika aononga dziko lino ndipo pofika 2019, a Malawi samvela ndi komwe nthano zimene a Mutharika angabwele nazo pa kampeni.

“Azanena kuti akufuna achite chani chimene chingasunthe a Malawi?” anadabwa a Chakwera.

“Mu zaka zinayi izi alephera kuchita kanthu, kuwaonjezela zaka zina kodi iwowa achitapo chani?” anaonjezelapo a Chakwera.

Kwabwela nyonga ku Kongeresi kuyambila pamene chipanichi chidabweletsa a Sidik Mia amene dzulo anakhala chifupi ndi a Chakwera.

Advertisement

20 Comments

 1. Ine siwandale koma our president has done more than good to this country restoring what mayi ena ake destroyed pa 10 minutes. I see no competitor trust me education and leadership move together. I need a leader not a pastor. Zavoteni mopepela muzaone

 2. Ask Malawi Assemblies of God Pastors about Wekwera.He is pompous and always wants to live a luxurious life.

  Every member of Malawi Assemblies of God was forced to contribute MK200 for the purchase of a Fortuner for his wife.Imagine poor agogos from villages contributing for purchase of a fortuner.This was 2013.What can stop him from reinforcing party cards if he forced church members to contribute MK200.No sane pastor in Malawi Assemblies of God can talk good about Wakwera,interview them and he personaly knows,he is a rough guy and corrupt through the church,then

 3. Kkkkkkk bwana chakwera fansani ndithu ndale ziri ngati mpira, nthawi zina umaganiza kuti timu ya kuti ndiyomwe ikangapambane pamathero ake koma zinthu zimasintha mwadzidzidzi choncho fansani ife amalawi tikuona mbali zonse ku chipani chanu ndi kuchipani cholamulacho cha DPP. Ndipo nonse azipaninu mudalila ife kuti tidzakuvotereni ndiye chondeee musamazithile mtchere kapena musamayankhule zambiri ai ndipo gwadani pansi mudzipempha kwa mwini zonse Namalenga, Mulungu chifukwa iye ndiamene akudziwa kuti inu Mr chakwera muwina kapena muluza ndipo izi palibe akudziwa koma yekhayo mulungu. Choncho wina asakunamizeni kuti mudzawina pofuna ndalama zanu ai dongosolo lili m’manja mwa mulungu basi.

 4. Koma ine sindikuona usogoleli mu mcp kut ungatukule malawi .. Iknw anthu azizavota chifukwa cha nkwiyo ndi agaist osaziwakut akuononga kwambili wait mcp munenayo iwine then muzaone mavuto azaoneni omwe zikolizizakumana nao jst wait. Lazalo mumukambayu alibe ndi expelience imene yolamulila koma yolalikila ndye dziko azalilamula bwanji.. B care amalawi

 5. Ife kwathu ndikudikira,mamuna ndani mu 2019.Tisamangonamizanapo apa.Pempho lathu:Chonde chonde ife ngati amalawi,sitikufuna kuzamva kuti wina wapita ku court kukasuma posagwilizana ndi zosatira.Tiyeni tizagwilizane ndi zosatira.

 6. Sometimes it helps to know the semantics and the context in which a phrase is used.In that instance you cant give literal translations because the interpretation changes.Nde inu a Malawi24 by saying kut DPP yagwilira Malawi, with the examples u hve given,wouldnt it have been clearer to kut DPP yaononga chuma,kayendetse/ulamuliro wabwino kuphatikiza kupsinja/kupondereza kukhazikitsa malamulo othandiza pa tsogolo la dzino? Nanga anthu adziti boma ndi munthu wot nkugwirira?

  1. Chakwera in his speech said that DPP has raped Malawi by among others plundering the state resources, poor governance etc.Nde muChichewa Malawi24 ikuti Chakwera wat DPP yagwiririra Malawi.

 7. Hahaaa ndale za kumudzi kwathu….. iiiiih. Tingogula president ngt mmene tinachitira ndi flames hope a Malawi’fe talepherana….

 8. Aaa ife si ana lazaro iwe uzakonza chani. Ndichoziwaziwa kale kuti nawenso udzamba kuzazitsa kaye thumamba lako. M’mene ukuikondela ndalama iwe chakwera asa.

Comments are closed.