Mahule akufuna chithandizo cha boma

Advertisement
prostitution malawi

Nawo ndi a Malawi ndipo atopa ndi zotsalidwa.

Tsopano akupempha kuti boma liwathandize kuti nawo azimva kuti ndi mzika za dziko lino.

Amayi oyendayenda auza boma kuti lisiye kuwayang’anila pansi ndi kuwathandiza kuti nawo azikhala ndi moyo osangalala mu dziko muno.

sex-workers-new
Amayi oyendayenda auza boma kuti lisiye kuwayang’anila pansi.

Iwo ananena izi mu boma la Ntcheu pamane anakumana ndi akuluakulu a bungwe la National AIDS Commission.

“Akakhala ogwila ntchito mu zipatala ndiye amatitenga ngati sife a Malawi ndi komwe. Akangozindikila kuti ndiwe mzimayi oyendayenda ndiye amatha olo kukana kukupatsa chithandizo. Ena ndiye amakuuza kuti agone nawe kuti akuthandize,” anamang’ala chotelo mmodzi mwa iwo.

Amayiwo anapempha kuti boma liwathandize ndi maphunziro okhudzana ndi ufulu wawo, ndi kuwapatsa upangili odziwa njira zothanilana ndi akuluakulu a boma amene amafuna kutengelapo mwayi oti iwo ndi mahule ndiye awachitile nkhanza.