Boma kudzera mu unduna wa zamasewero latsimikizira anthu okonda masewero a mpira wa miyendo kuti bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre litsegulidwanso mu mwezi wa Okutabala.
Watsimikiza izi ndi nduna ya zamasewero a Francis Kasaila yemwe wati boma likugwiragwira kuti bwaloli alitsegule msanga.
Bwaloli linatsekedwa kuti likonzedwenso kamba koti malo okhala ochemelera ndi owonongeka kotero amayika miyoyo ya anthu pa chiwopsyezo.
A Kasaila ati boma linapereka ndalama zokwana 1.5 billion kwacha mu ndondomeko ya za chuma ya chaka chino zokonzekera bwaloli.
Malingana ndi ndunayi, ndalamazi agwiritsira ntchito pokonza malo omwe anaonongekawo komanso kuika kapinga wina wa makono.
Poyamba panali mtsutso pomwe panali ganizo loti bwalo la zamaseweroli aligwetse kuti pamangidwe lina latsopano pamene ena amati bwaloli asaligwetse koma boma limange bwalo lina mu mzinda Blantyre.
Bwalo la zamasewero la Kamuzu linamangidwa m’chaka cha 1959.