Dalaiva, kondakita amangidwa chifukwa chonyamula ma 4 – 4

Advertisement
cuffs

Ku Phalombe, Dalaiva wina wa minibus ndi kondakita wake atsekeledwa mu chitolokosi kamba konyamula anthu ngati matumba a mbatata.

Apolisi mu bomalo ati atsekela awiriwo kamba koti ananyamula anthu makumi awiri kudza mphambu zinayi (24) mu minibus imene inapangidwa kuti izinyamula anthu khumi ndi asanu ndi mphambu imodzi (16).

“Ananyamula ma folo folo pampando, kuwapanga anthu ngati matumba. Anayika moyo wa anthu pa chiopsezo,” anatelo Apolisi.

Awiri atsekeledwawo ndi a Steven Lawrence a zaka 34 ndi a James Bwanaisa a zaka 29. Iwo anali mu minibus ya  Nissan Caravan.

Aka ndi koyamba kuti Apolisi mu boma la Phalombe amange anthu kamba koswa malamulo a pamseu.

 

Advertisement

64 Comments

 1. Koma mw sizatheka chikwama chomwe wanyamula munthu sunawikeso pa mpando pokhala wanthu kudula mtengo kuposa iwe munthu komaso kunyamula anthu 30 malo mwa 15 chisoni kuba basi

 2. Umbuli wa Amalawi ndi wamtundu wosiyana ndi wa m’maiko pa Dziko lonse. Timawoneka ngati osazindikira pakuyankhula koma chonsecho maganizo ali obwerera mbuyo kotheratu. Sikale ayi m’mene ma Dalaivala ndi ma Kondakitala awo anazunza Anthu chifukwa cha kusafuna kuvomera kulemekeza Malamulo komanso okwera Basi. Pofuna kukwaniritsa zowona zawo mosalabadira Anthu, adakweza mitengo yolipirira maulendo ndiye poti ku Malawi Anthu amatheka kuseweredwa ngati Mpira, mitengo yowonjezeledwa tidaivomera. Lero lino potiwona kukhala ombwambwana ayambanso kutilongedza ngati matumba pa mitengo yokwera yomweyo. Amalawi anzanga, timati ndiife a makono chonsecho, tulo ntachikhalire, kapena tidziti mademo ndipamene timawona ngati kuchenjera?.

 3. Kuno ku Makwasa Vannet timakwela anthu 36 (Thirty six ena pamwamba pa Minibus.
  Ndipo vuto palibe bola mateyala apopedwe bwino, ulendo ulipo.
  Cheers

 4. Mudzamvetsa chifukwa chonyamulira anayi pampando uliwonse mukadzagula yanu Minibus. Apa mungobwebwetuka chifukwa simumvetsa za business ya Minibus.

  1. Business yomangoganiza za phindu lako lokha osaganiza za miyoyo ndi ufulu wa anzako? Ngati kunyamula atatu pa mpando kulibe phindu osangogulisa maphaphawo mkukayamba ya phwetekele bwanji?
   Za ziiii

 5. Zopanda nzeru anthu amalora chifukwa chosowa ma bus okwera boma kudziwa kumanga koma njira yothana ndi mavuto osadziwa boma lipeze Ma basi liponye Ma boma onse lizipanganawo business anthu sitingakwele 4-4 Ma bus ali mbweeee kolo likamaletsa ana kudya kwa eni kumafunika kupeza chakudya chokwanila pa khomopo akamakanikabe Ndiye timapeleka zilango

 6. mmmmm, ai, tiyeni tiziyankhula zoona, tisamanene kuti tioneke ngati ndife angelo matumba ambatata mukuwaziwa? inu? mungafanizile ndi munthu tiziweluzana choncho kusekelana kumangidwa, koma dziwani kuti lilipo tsiku lalikulu lomwe oweluzayo azaweluzidwe molingana ndi maweluzidwe a momwe anaweluzila pansi pano, omanga anzao chimozimozi, tizingoyang’ana zikamachitika tili m’asiku ena ano.

 7. Mubwereso kunokumpoto anyamata akaronga amachitazomwezo koma palibe chazeru chomwe atrafic akupangapo ayi while mitengo anakweza basitizikweraso 4-4zowona

Comments are closed.