A Malawi ndiwo akutsogolera kupha anthu a danzi ku Mazambiki

Advertisement
Mozambique Bald Men Attacks

Apolisi a mu dziko la Mozambique ati ziwembu zimene zikuchitika kwa anthu a danzi mu dzikomo akuziyambitsa ndi a Malawi.

Mozambique Bald Men Attacks
‘A Malawi ndiwo akutsogolera kupha anthu a danzi ku Mazambiki’;

“Akukhulupirira kuti mu danzi muli golide, ena ati muli mankhwala olemeletsa,” atelo a Polisiwo pouza nyumba youlutsa mawu ya BBC.

Apolisi amenewa aonjeza kunena kuti Anthu amene akuchita upandu anthu a danzi, ndi anthu ochokera mu dziko lino la Malawi ndinso ena ndi a ku Tanzania.

“Pali ena a komwe kuno ku Mozambique koma ambiri akuchoka ku Malawi ndi ku Tanzania,” atelo a Polisi a kumeneko.

Iwo aululanso kuti tsopano mu dziko la Mozambique mwakhazikitsidwa nthambi ya Apolisi kuti iteteze anthu a danzi.

“Sitikungokhala iyayi, pano kuli nthambi ya pa dera yoti iziteteza anthu a danzi.

Malipoti oti anthu adanzi akuchitidwa chipongwe anatchuka mwezi watha kuchoka mu dziko la Mozambique.

Pofika pano zadziwika kuti Anthu asanu aphedwa ku Mozambique kamba kokhala ndi danzi.