A Malawi ndiwo akutsogolera kupha anthu a danzi ku Mazambiki

Mozambique Bald Men Attacks

Apolisi a mu dziko la Mozambique ati ziwembu zimene zikuchitika kwa anthu a danzi mu dzikomo akuziyambitsa ndi a Malawi.

Mozambique Bald Men Attacks
‘A Malawi ndiwo akutsogolera kupha anthu a danzi ku Mazambiki’;

“Akukhulupirira kuti mu danzi muli golide, ena ati muli mankhwala olemeletsa,” atelo a Polisiwo pouza nyumba youlutsa mawu ya BBC.

Apolisi amenewa aonjeza kunena kuti Anthu amene akuchita upandu anthu a danzi, ndi anthu ochokera mu dziko lino la Malawi ndinso ena ndi a ku Tanzania.

“Pali ena a komwe kuno ku Mozambique koma ambiri akuchoka ku Malawi ndi ku Tanzania,” atelo a Polisi a kumeneko.

Iwo aululanso kuti tsopano mu dziko la Mozambique mwakhazikitsidwa nthambi ya Apolisi kuti iteteze anthu a danzi.

“Sitikungokhala iyayi, pano kuli nthambi ya pa dera yoti iziteteza anthu a danzi.

Malipoti oti anthu adanzi akuchitidwa chipongwe anatchuka mwezi watha kuchoka mu dziko la Mozambique.

Pofika pano zadziwika kuti Anthu asanu aphedwa ku Mozambique kamba kokhala ndi danzi.

Advertisement

155 Comments

 1. Aaah,Malawi tiyeni tichenjere ndithu adani ndi ambiri too achuluka ku northern part a tanzania akufuna atilande nyanja apa mozambique ikutiso ndife timayambisa chiwembu muziko mwawo,, kodi mwina 2 nations angopangana kuti awone kuyipa kwathu?

 2. Not totally Malawians, Bt thy,should say SOME malawians ar taking part; Coz in the issue of albinos, Some unpatrioric Malawians were involved. So lets just condemn the Malplactice May Be by sentencing to death Those found Guilty…

 3. Sizinati, these are end times, expect the worst, coz Satan’s days are few. My advice , pray to God all the time and he will preserve u

 4. Akupha okha anthu adazi nkumanamizira kuti ndi amalawi.Apatu ndi nsanje basi malawi tiyenela kuchenjela mafulelimo ndi malenamo kapena tingoti aphwitikizi yawo ndi nkhondo basi wathu m,bale ndi Zambia.

 5. mawu amulungu akuti uzadya thukuta lako bwanji tikutha azathu pofuna ulemera zulo alubino lero adazi mawa amphwi onse mulungu langani oterowo

 6. apa nde ndazindikira kut Neba wathu wokondana naye ndi Zambia basi coz enawa akut tikutsongolera kupha anthu adazi, mbali inayi akut nyanja yathu ija ndiyawoso YYY????

 7. Mitu ya anthu aku Mozambigue simagwira ntchito utsi wa mifutu ya nkhondo ankapanga ija idawasokoneza panopa kungot onse nd openga ndye sangafunire anzao za bwino

 8. Kunama Anthu Akugolongoza ”Kumpanyira”Kumoshiko”Akutifuna Kut Tiyesenawo Zida. Kkkkkk

 9. Thats faken mocambique amalawinso tili ndi anthu akazi ambirimbiri bwanji sakumapha aku malawi konkuno kunena zoona mwatopa kumenyana nokha nokha pano mukufuna muyambane ndi amalawi anthu oipa opanda chisoni a potigisi ndipo tikatengela mbiri ya moshico ndili dziko lokonda ufiti chifukwa sizingatheke mulungu kuika gold mwa adazi kumeneko okha whill aku malawi ndi Tanzania osawayika limenero ndiye bodza komanso zikusowe umboni okwanira kuti mwawagwira amalawiwo osati khamba kamwa chabe

 10. Nkoonatu anati zizirisira plan ya doko poona kuti amalawi ndima hard worker
  Akufuna atamangise amalawi onse kwinaku akuwabela. Asawaziwa ndindani

  1. FUNSO LA NZERU NDI LIMENE AFUNSALO: “AGWIRAPO ANGATI AKU MALAWI?? KODI ALIBE MAINA?? CHIFUKWA YOTELEYI YAYENELA KUTI IDALOWA M’KHOTI KUTI ADZIWEDI NDI AMALAWI AKUPHA ANTHU A DANZI!!

 11. Pa zikhala umboni okwanira owayimbira a Malawi ali ku Mozambigue kuti ndi amene akupha anthu adanzi osangopanga flame a Malawi pa nkhani zoduka mutu ngati iziii .

 12. Amalawi tichenjere, apapo, angofuna kutionongera mbiri yachikhalidwe chathu, monga amalawi, chifukwa sizingatheke amalawi kulowa m’Mozambique ndikukapha antu adazi, pomwe Ku Malawi ko, adazinso aliko, akuphana okhaokha kumeneko, bwanji, amango ulusa mpekesera, m’malo mogwira anthuwo, kuti papezeke umboni weniweni, kuti ndi Amalawidi akupha antu kumeko, akufuna chiwembu Malawi isamale pamepa!!!

 13. MBUZI ZA KU MOZAMBIQUE KUTIONELELA ETI?? AIWALA KUTI AKHALA AKUPHANA ZAKA 17, APA AKUFUNA KUTIPAKA NAWO VUMBA LIMENELI AKAGWELE.

 14. Kuyankhula koti amalawi ulesi,ndikuyankhula mopusa kapena kuti kuyankhula mauchibulutu.Iweyo upite ku Mozambique ko ukamgwire mmalawi amene aliwaulesi komanso akuyambitsa zotelezi ubwele nawo.Sichina iyayi koma omwe anatiphunzitsa ife amalawi ulemu sanatiuzenso kuipa kwake,mchifukwa amalawi ambiri ndiopusa pakuyankhula ngati uku.M’malawi siwaulesi,amene akuti amalawi akuyambitsa zotelezi ndiye awagwire amalawiwo atitumizire tiwaone.

 15. Koma inu !!!! eishiii!!! mbuyomu timanva za alubino pano anthu adazi , satanatu ameneyo , ndiye zikusiyana pati muthu wadazi ndi wopanda dazi sichimodzi modzi muthu akameta tsitsi? Ambuye bwerani muzaweruze zikoli satana wadzela ku ndalama .

 16. aziwapha so nawo a malawi wo osamawamanga siakupha anthu azilawa mpeni so osanyengelela kodi malamulo akamuzu aja bwanji kuwabweletsa poyela amene aja zitha kusinthako wexi akuxiopa ng.ona kukazidula maliseche muzambezi mo ati koma Ku dazi ndekuli chidule I phani a Malawi Ku Mozambique ko Ngati achoka kuno nkumakapha Ku meneko sia malawi ameneyo amangotha chabe chilankhulo chathu iphani ndithu kumawa phelaso mateyala petro ndio tchipa kale otchani ndithu fire fire

 17. surprised? iwouldnt b surprised, thy are experienced from the killing of albinos, whn the law enfocers were jst quite… in the country

  1. even if thy are killing innocent souls? ushould b mad,imagine its u or ur relatives geting killed jst cz ndi albino or ali daz……. share the filing wth those who lost thr loved ones and lives unlike sympathising wth murders. Nosence jail is thr to punish such pple and ur blaiming jst a statement!!

 18. Kuyambira kalekale palibe ubale ku maiko awiriwa ngakhale Kamuzu Banda ali moyo Mozambique ndi malawi panali udani kale,Mozambique ndi dziko lodzikonda kwambiri anakana kuti malawi ipange chitukuko kudzera ku mozambique,analimbana ndi malawi mu zaka zambuyomo mbali ya malo,koma chimene amayiwala ndichakuti akayambana okhaokha anthu awo amathawira ku malawi kukakhala ma refugees,pano akupha anthu amadazi kwaoko akuti ndi amalawi akupanga zimenezo koma ayiwala kuti ufiti umatchuka kwambiri ku mozambique kwao komweko,Malawi uzikhala ochenjera chifukwa tikukhala pafupi ndi adani anthu pafupi.Zambia ndi dziko lokhalo limene limagwilizana ndi Malawi basi koma maiko ena onsewo samufunira malawi zabwino.God continue bless these two countries #Zambia and Malawi

  1. man ndizoona agwidwa anthu six awiri akwathu ku Malawiko, awiri eni ake akuno, pamene ena osalawo maiko akwawo sakuziwika, amene sakuziwikawa aphedwa masiku apitawa.

  2. Chifukwa chakuti Ku Zambia kuli achewa, atumbuka, atonga komanso angoni ndiye timafanana zikhalidwe.timayankhulanso chilankhulo chimodzi.

  3. Ndikuyankhe pang’ono zaudaniu,nthawi imene frelimo ndi renamo amamenyana boma la Malawi limathandiza renamo amene anali oukira,choncho chipani cha frelimo chikulamulira mpaka lero ndiye limaona kuti timasungira adani awo.

 19. umboni woti akumayambitsa ndamalawi ali nawo ? komaso agwirapo angat amalawi wo , meaning kut kumalawi kulibe anthu adazi kut paka akafike kumozambiq , asatiyipitsire dziko lanthu zimenezo akuzichita okha ,akutanzaniawo ndikhalidwe lawo lofuna kuleremera, akagwele uko ,akanagwira awiri or modzi ngat umboni

 20. Bwino muziona nkhani zopanga gossip, Do you think ayini ake aku Mozambique atamva angazitenge lightly? Mudzapetsa anthu osalakwa.

Comments are closed.