Neba sizikuyenda: 1 pa 6 kwa Bullets, 6 pa 6 kwa Noma

Advertisement
Be Forward Wanderers

Timu ya mpira wa miyendo Nyasa Big Bullets ikupitilirabe kusachita bwino mu TNM super league pomwe yakwanitsa kutenga point imodzi yokha mchigawo chapakati mumasewelo awiri.

Bullets idalephera kugonjetsa timu ya Blue Eagles pa Bwalo la Nankhaka loweruka lapitali mu mzinda wa Lilongwe ndi chigoli chimodzi kwa chilowele.

Be Forward Wanderers
Be Forward Wanderers zawo zikuyenda.

Timu yafukoyi ikuoneka ngati sidapezebe njira yokhazikika yowinila italepherana ndi timu ya Master Security imene yangolowa kumene mu ligiyi posagonjetsana chigoli chilichonse pa bwalo la masewelo lalikulu mu mzinda wa Dedza.

Pa masewelo awo asanu ndi awili amene anyamata a Nswazurimo Ramadhan asewela akwanitsa kupeza ma points khumi ndi imodzi zomwe zikuwaika panambala yachitatu pa ndandanda wama team mmene akuchitila mu league yaikulu mdziko munoyi.

Bullets ikutsatanatsatana ndi timu ya Wizards yomweso ili ndi maponits khumi ndi imodzi ngakhaleso yasewela ma game asanu ndi imodzi.

Neba wa Bullets, Be forward Wanderers yamwetsa ochemelera ake wankaka mathelo omwe Bullets yawona zowawayi itakwanitsa kutenga ma points onse asanu ndi imodzi chigawo chapakati zomwe zapangitsa team imeneyi kukhala pa nambala yachiwili pa mndandanda wa ma team a mu ligi wa.

Manoma ali pa chikondwelero chifukwa yakwanitsa kupambana masewelo anayi omwe ansewela. Manoma ikufanana mapoints ndi mikango yaku Zomba, Red Lions yomwe ili pamwamba pa TNM koma yasewela masewelo asanu ndi imodzi.

Padakali pano ma team atatu okha ndi amene asewela masewelo asanu ndi awili ndipo Big Bullets ili mguluri.

Umu ndimmene mateam achitila mathelo asabata yapitayi: Loweluka Silver strikers yagonjetsa timu ya Chitipa united ndi zigoli kwa chilowele, Azam Tigers ndi Blantyre United agawana point atalephelana zigoli zitatu aliyense, Bullets idaluza kwa Blue Eagles ndi chigoli chimodzi kwa palibe, Manoma idapambadza Dwangwa United ndi chigoli chimodzi kwa palibe ndipo team ya Kamuzu Barracks idagawana point ndi team ya Civo Sporting Club atagoetsana chigoli chimodzi chimodzi.

Lamulungu timu ya Manoma idapitiliza kudzodza mateam zigoli pomwe idagonjetsa asilikali aku Zomba ndi zigoli zitatu kwa chilowele, Bullets idalepherana ndi Masters Security posagoletsana chigoli chilichonse.

Masewelo a Silver Strikers ndi Moyale Barracks adaliso opanda zigoli.