Akuba afukula manda ndikudula sidze, zikope za mtembo

Advertisement

Munkhani yovetsa chisoni, akuba sabata yatha m’boma la Mchinji anafukula manda ndikudula zikope komaso sidze za mtembo.

Malingana ndi malipoti a polisi, nkhaniyi inachitika mmudzi mwa Kadula Malambo mfumu yaikulu Mlonyeni m’bomalo ndipo anthu akuganizila kuti izi zinachitika usiku wa la chinayi pa June 14.

A polisi ati manda omwe anafukulidwawo ndi a Dalitso Zulu wa mmudzi momwemo yemwe anatisiya pa 11 June ndipo mtembo wake unaikidwa mmanda pa 12 lomwe linali tsiku lotsatila.

Chomwe chinatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga mchakuti anthu ena omwe amadutsa munjira yomwe inalambalala mandawa anagwidwa ndimantha othetsa mankhalu ataona manda a malemu Zulu ali ofukulidwa.

Podziwa kuti mutu umodzi suseza denga, anthuwa anakauza zamalodzawa anthu ena omweso anakabenthulira za nkhaniyi amfumu ammudzimo omwe ose anatengana kukaona za malodzazo.

Atafika kumandako kunali mfuu yakulira kwa azibale komaso amzake a malemoyo ataona kuti mandawo analifi ofukulidwa ndipo aliyese anali wachisoni ndipo anakumbuka padzana ali limodzi ndimalemuwo poti panali patangotha masiku awiri chimwalilireni.

Mfumu yammudziyi nayoso inagwidwa ndichisoni ndipo anali kakasi kusowa chochita koma akulu ndi mdambo mothera moto ndipo anakaisiya nkhaniyi kupolisi.

Mosazengereza apolisiwa anafika pamalopa ndipo anautengera mtembowo Ku chipatala cha chikulu m’bomali komwe anakauyeza.

Zotsatira zakuvhipatalaku zinaonetsa kuti ziwalo zina pa mtembowo zinali zitadulidwa ndichipangizo chakuthwa kwambiri chomwe akuchipatalawo akuganizira kuti ndi lezala.

Achipatala atsimikiza kuti anthu omwe anachita izi anadula zikope zonse komaso sidze pa thupili.

Padakali pano, apolisi ati akhazikitsa kafukufuku Lusaka zifwamba zomwe zinavhita zachipongwezi ndipo ati Ali ndivhikhulupiliro kuti zifwambazi zigwidwa posachedwapa.

Aka sikoyamba kuti zinthu zamtundu uwu zichitike mdziko muno koma kwambiri zimachitika kwa anthu omwe anatisiya a mtundu was chialubino.