“Hallo! Ndi kumwamba kumeneko…ndilankhu­leko ndi Mulungu,” m’busa alankhulana ndi Mulungu pa selefoni

Advertisement
Pastor Paul Sanyangore

Masiku otsiliza mudzaona zinthu zosiyanasiya zina zoona komanso zina zomusemera Mulungu koma iye asananene kalikonse mkamwa make, malemba amatero mu buku lopatulika.

Izi zikupherezera pamene m’busa wina m’dziko la Zimbabwe akuti walumikizana ndi mulungu osati mu pemphero koma pa foni yake ya m’manja.

Pastor Paul Sanyangore
Abusa Paul Sanyangore kulankulana ndi Malungu pa lamya.

Mmalingana ndi ka vidiyo kamene Malawi24 yawona, kakuonetsa m’busayu yemwe dzina lake ndi  Paul Sanyangore mpingo wa victory world international ministries akuti akulankhulana ndi mulungu pa foni pamaso pa khwimbi la wanthu mkachisi.

Ka vidiyoka komwe kawanda kwambiri pa masamba a mchezo pofika lolemba pa 22 March kadali katawonedwa ndi anthu okwana mazana 77 pa tsamba la mchezo lija lotchedwa You tube. Ndipo kakuonetsa m’busayu ali ndi mzimayi ovala zovala zoyera ali kutsogolo manja ake ali okweza atagwada pamaso pa m’busayu.

M’busayu akumveka ndi kuoneka akumufunsa Mulungu kuti alankhule chani kwa mzimayi yemwe wagwada pa patsogolo pake ndipo waoneka akumvetsera modekha kusonyeza kuti wina akuyankhulana naye pa foni yake ya mmanjayo.

“Halloo! Kodi ndi kumwamba kumeneko?, kodi ndiyankhulenji kwa mzimayi amene ndili naye panoyu?” (Hello, is this heven? I have a woman here, what do you have to say about her) Adafunsa m’busa pa foni pake.

Mpingo onse mosakhulupilira ukuoneka ozizwa komanso idabwa kwambiri ndi zomwe m’busayu wachita. Pamene mnyamata wina akumveka akuyankhula mozimuka kuti “oooh Mulungu alemekezeke”

Povomereza zoyankhulidwa pa foni, Paul wamveka akuvomereza kuti “ooh ok ndimufunse kuti Sibo ndi ndani?” Anayankhula m’busayu.

Atafunsa iye kuti Sibo ndi ndani? anaoneka akulankhulanso pa foni kumufunsa uyo amayankhula nayeyo kuti anene chinachani mzimayiyu, ndipo anamufunsa mzimayiyu kuti “mchifukwa chiyani
Akundionetsa mtima” ndipo ziyankha za mzimayiyu sizinamveke popeza amayankha monong’ona.

Mulungu akuti tipempherere ana ako onse awiri, akuti m’modzi ndi odwala khunyu ndipo wina ndi wa matenda obanika kupuma” (he says we should pray for your children, two of them, he is saying one is epileptic the other one is asthmatic) adauzidwa mzimayi.

Anthu ambiri a mumpingiwu awoneka akusangalala kutamanda mtumikiyu pochita zodabwitsa kulankhulana ndi mulungu pa telefoni ndipo analankhula mwa thamo kuti kumwamba kukupezeka pa foni (heaven is here) ndipo anauza mzimayiyu kuti nyengo zake zasintha.

Komabe izi zadzetsa mafunso ambiri ndipo anthu enanso a mu mpingowu sakukhulupirira kuti izi mzowona.