A Malawi 300 ayenda wa uyo uyo ku Joni

Advertisement
South Africa Police

Nzika za ku Malawi zokwana 300 zomwe zimakhala m’dziko la South Africa koma opanda zikalata zokwanira azitumiza kuno kumudzi.

Potsimikiza za nkhaniyi, wachiwiri kwa m’neneli wa nthambi ya boma yowona zotuluka ndi kulowa a Wellington Chiponde ati theka la anthuwa lafika kale kuno kumudzi lachiwiri kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu ku Lilongwe.

Malingana ndi a Chiponde, anthu okwana 150 afika m’dziko muno ndipo ena akuyembekezeka kufika masiku akubwerawa.

Iwo anaonjezera kuti pamene anthuwa akufika kuno kumudzi, athu ena okwana 849 awambwandila ndipo akusungidwa chifukwa chosatsatila ndondomeko zofikira ndi kukhalira m’dziko la chilendolo.

Chiponde wachenjeza a Malawi kuti azitsata ndondomeko ndi malamulo otulukira m’dziko muno kupita ku mayiko a kunja popewa kubwezedwa mokakamiza, mwa chipongwe ndi mochotsa ulemu.

“Tikupempha a Malawi kuti adzitsata ndondomeko ndi malamulo oyendera nthawi zonse, kukhala ndi chiphaso sikokwana koma kudziwa zonse za zomwe dziko lililonse lomwe akupitalo limafuna pa anthu onse olowa m’dzikomo,” adalankhula choncho a Chiponde.

A Malawi ambiri amalowera ku South Africa komwe amakasaka mwayi wa ntchito, ndipo choopsa kwambiri ndi choti amalawi ena amadzera njira za chidule komanso opanda zikalata zoyendera pa ulendo kupita ku dzikolo.

Pafupifupi chaka chilichonse boma la Malawi limaononga ndalama zochuluka kubweretsa anthuwa kuno kumudzi ku South Africa kukasokonekera kapena akathothedwako mwa chikhadzakhadza zomwe zimasokoneza ndondomeko ya za chuma cha dziko lino ngati silidaike ndalama zapadera.