Ma timu ndidziwaphera nzeru osati mphamvu – Joseph Kamwendo

1

Osewera mpira wa miyendo yemwe ndi m’modzi mwa a chiyamba-kale m’dziko muno, Joseph  Kamwendo wati iye akukula koma mu maseweredwe ake a mpira ma timu adziwaphera nzeru.

Kamwendo yemwe pakali pano akusewera mpira wake mu timu ya Be Forward Wanderers wati zokamba za anthu kuti iye maseweredwe ake adasintha sizikumukhudza popeza nzeru imaposa mphamvu ndipo wauza anthu kuti aliyense asamuyikire malire a mpira wake.

Be Forward Wanderers

Joseph Kamwendo: Ndipanga zinthu.

Poyankhula lachiwiri pa wayilesi ina m’dziko muno, Kamwendo yemwe anabadwa m’chaka cha 1986 anati nzeru zomwe iye ali nazo mu masewera a mpira wa miyendo zikusiyana kutali ndi za iwo amene akuyaka moto kudzera mu mphamvu zawo.

“Chinthu chimodzi chakuti mudziwe ndi choti nzeru imaposa mphamvu, enawo inde atha kukhala ndi mphamvu kuposa ine koma ine ndidzigwiritsa ntchito nzeru, ndipo ma timu ndidziwaphera nzeru,” watero Kamwendo.

“Ndipo ntchito ndigwira chifukwa ine ntchito yanga ndi yosewera mpira, olo musandipatse chilichonsecho, olo musandiyike mu timu mwanu koma ine ntchito yanga ndi yokankha chikopa ndipo ndigwira ntchito,” adaonjezera m’mawu ake.

Osewera wa zaka 31-yu wati iye amamva kukoma kwambiri akamasewera mpira makamaka ku timu ya Wanderers yomwe adalowa atachoka ku timu ya Civo United mu chaka cha 2003, ndipo watsindika kuti iye adzasewerera timuyi monga wakhala akuchitira ikusowa thandizo kapena kukhala ndi thandizo.

Joseph yemwe ndi wosewera pakati mu timu yayikulu ya dziko lino komanso Manoma wakhala ali otsogolera anzake m’bwalo la zamasewero zomwe zimamulimbikitsa kuti ali ndi kuthekera mu nzeru.

Kamwendo anayamba kusewera mpira mu timu ya dziko ali wachichepere kwambiri ndipo wakhalanso akusewera m’matimu a kunja kwa dziko lino monga; Orlando Pirates, Vasco Da Gama, LD Maputo, TP Mazembe, CS Don Bosco ndi CAPS united ku Zimbabwe komwe m’chaka cha 2005 adakhala osewera oyamba wapamwamba kwambiri ochokera dziko lina ndipo adalandila mphoto.

Share.

One Comment

%d bloggers like this: