Inu a kumpoto, iwalani za u President – yatelo DPP

Advertisement
dpp

Ngati muli a chigawo cha kumpoto ndiye mumakhumba kukhala President ndiye kuti ndinu munthu wa chibwana kwambiri.

Greselder Jeffrey
Greselder Jeffrey: Akuti ku mpoto sikuzatuluka mtsogoleri wa dziko.

Malinga ndi mlembi wamkulu wa chipani cha DPP  Mayi Grezzeder Jeffrey wa Jeffrey, palibe munthu wa kumpoto angakwanitse kukhala mtsogoleri wa dziko lino.

Mayi Jeffrey anena izi pa msonkhano umene anachititsa.

Pa msonkhanowo Mayi Jeffrey anapezelapo danga lothila ukali Bambo Frank Mwenifumbo amene alowa chipani cha AFORD.

“A Mwenifumbo ndiye ndi omvetsa manyazi, nanga munthu wamkulu lero ndi kumapita ku AFORD?” analankhula motero.

“Ife a DPP tinawauza abwele mbali yathu, koma iwo kukana ndi kupita ku AFORD. Kodi ngati anakanika u President ku AFORD a Chakufwa Chihana, a Mwenifumbo angautenge?” iwo ananyogodola.

Pofuna kuonjeza chipongwe, Mayi Jeffrey anauza anthu kuti chigawo cha kumpoto sichingakwanitse kutulutsa President chifukwa kuli anthu ochepa.