Khoti lisekelela Bambo ogwililira nkhalamba ya zaka 80

Advertisement
Machinga

Ngakhale chilango cha munthu ogwililira chili moyo onse kundende kapena kunyongedwa kumene,  Bambo wina wangogamulidwa miyezi yochepa chabe ngakhale anachita chipongwe gogo.

Malinga ndi ma umboni mu Khoti, Bambo Biwi Ephraim a zaka 54 anagwililira gogo wina wa zaka 80.

CourtIzi zinachitika mmudzi mwa Chifisi, mu boma la Dowa.

Malawi24 yamva kuti tsiku limene Bambo Ephraim anachita chipongwe gogoyu, iye amachoka ku mowa.

Ati a Ephraim atamuona gogoyu kuzandila, iwo anayamba kumulondola. Iwo atafika pamalo ena achete, anamukokela patchire gogoyu ati ndi kumuchita chipongwe.

Nkhaniyi itafika pabwalo la majisitireti, ati Bambo Ephraim anakana kudziwapo kanthu pa chipongwe anachitidwa gogoyu. Koma a boma anabweletsa mboni zochuluka ndipo pamapeto pake Bambo Ephraim anapezeka olakwa.

Iwo podandaula, anapempha a Khoti kuti asawalange kwambiri ati chifukwa iwo ndi achikulire.

Koma a mbali ya boma anapempha bwalo kuti lipeleke chilango chokhwima kuti ena atengepo phunziro.

Zodabwitsa kwambiri, majisitireti pogamula anawauza a Ephraim kuti basi akagwile ya kalavula gaga kwa miyezi makumi atatu.