Khoti lisekelela Bambo ogwililira nkhalamba ya zaka 80

Advertisement
Machinga

Ngakhale chilango cha munthu ogwililira chili moyo onse kundende kapena kunyongedwa kumene,  Bambo wina wangogamulidwa miyezi yochepa chabe ngakhale anachita chipongwe gogo.

Malinga ndi ma umboni mu Khoti, Bambo Biwi Ephraim a zaka 54 anagwililira gogo wina wa zaka 80.

CourtIzi zinachitika mmudzi mwa Chifisi, mu boma la Dowa.

Malawi24 yamva kuti tsiku limene Bambo Ephraim anachita chipongwe gogoyu, iye amachoka ku mowa.

Ati a Ephraim atamuona gogoyu kuzandila, iwo anayamba kumulondola. Iwo atafika pamalo ena achete, anamukokela patchire gogoyu ati ndi kumuchita chipongwe.

Nkhaniyi itafika pabwalo la majisitireti, ati Bambo Ephraim anakana kudziwapo kanthu pa chipongwe anachitidwa gogoyu. Koma a boma anabweletsa mboni zochuluka ndipo pamapeto pake Bambo Ephraim anapezeka olakwa.

Iwo podandaula, anapempha a Khoti kuti asawalange kwambiri ati chifukwa iwo ndi achikulire.

Koma a mbali ya boma anapempha bwalo kuti lipeleke chilango chokhwima kuti ena atengepo phunziro.

Zodabwitsa kwambiri, majisitireti pogamula anawauza a Ephraim kuti basi akagwile ya kalavula gaga kwa miyezi makumi atatu.

Advertisement

56 Comments

  1. Ngati Akuti Gogoyo Wasangalara Chifkwa Choti Ananyengedwa Kale Zaka 80?, Mwinaso Kumaliseche Kwa Gogoyo Kunabwera Akangaude Zimbiliyo Ndipang’ono Pamenepo, Komaso Bamboyo Amafna Kusiyanisa kukoma Kwa Kale Ndi Zaka Zino

  2. Nayetso paka kugwirila Nkhalaba mwina munthu wake tsukugwira ntchito. Momwe Ma hule achulukiramu otsagofutsila bwanji hule

  3. Ndani ogwililira adapatsidwako chilango chokhala moyo wonse kundende kapena kunyongedwa ku Malawi kuno? Chakwana chilango chimenecho ndipo miyeziyo yachulukanso. Bwanji osamamanga azibambo okula zimimba amabanja awo omwe akusokoneza tiwana ta school ndi ndalamawa?

  4. Akuti khoti lachita izi chifukwa linauzidwa ndi Gogo yo kunena kuti munthuyo sakuyenela kupatsidwa chilango chachikulu chifukwa chakuti gogoyo inali yosangalara pakuona munthu wachifundo amene anaikumbutsa kale lawo

    1. Ndiye pali chifukwanso pamenepa, chomutengera munthu ku court? Ngati mwini wake akusangalala kuti, wandikumbusa kale langa. Anaitumiza nkhaniyi ku court, ndindani nayenso timutsekulire mlandu?

    2. Wadandaura kale gogoyo akuti kwa iyeyo sakuonapo chifukwa chomutengera ku court m’bamboyo, chifukwa samangitsa munthu osalakwa. Anapitilizaso kunena kuti abale akewo sakumufunira zabwino mgogoyo pamudzipo

Comments are closed.