Musamange mahule – Khoti liuza apolisi

Advertisement
prostitution malawi

Apolisi a vakabuali pa chi ntchito choopsa pamene alamulidwa ndi a khoti kuti asiyiletu mchitidwe omanjata azimayi oyendayenda usiku ati chifukwa kutelo ndikuwaphela amayiwo ufulu komanso ndikulakwila malamulo a dziko lino.

Malingana ndichigamulo chimene khoti lalikuluku Zomba lapeleka, a polisi alibe mphamvu yomanga amayi Kamba kot iawapeza mu malo omwela mowa kapena achisangalalo, ngakhale ogona alendo.

sex-workers-new
Amayi oyendayenda apeza ‘ufulu’

Oweluza milandu a mayi ZioneNtaba anagamula izi amayi ena oyendayenda atakamang’ala kubwalo la milandu kuti ananjatidwandi a Polisiati Kamba kopezeka kuti akuyendausiku.

Amayiwa atanjatidwa mu boma la Dedza, anapititsidwa kubwalo la milandu laling’ono kumene anapezeka olakwa.

Koma iwo posakhutitsidwa ndichigamulo cha bwalo laling’ono, anathamangila kubwalola likulu kumene a bwalo anagwilizananawo.

Malingana ndi akuluakulu a zamalamulo m’dzikomuno, mchitidwe wauhule si mlandu m’dzikomuno ndipo palibe ndime imene imanena kuti kugulitsa thupilako munthu ukuyenela kulangidwa.

Nthawi zambiri a Polisi amanjata anthu oyenda usiku ati pa mlandu opezeka oyenda opanda chifukwa pa nthawi yolakwika.

Nthawi zambiri apolisi akagwila amayi oyenda usiku amagona nawo mowakakamiza kuti awatulutse.