15 September 2016 Last updated at: 11:37 AM

Msonda azitaya, atuluka PP

Chipani chija chikutha anthu akuona.

Mneneri wachipani chostutsa cha Peoples’ amene anakakamila ngalawaya chipanichi ngakhale mtsogoleri wake atachithawa, a Ken Msonda, alengeza kuti basi iwo alekana nacho chipanichi.

A Msonda analengezaizi pa tsambalawo la pa Fesibuku kuti tsopano iwo simmodzi mwa anthu a mu chipanichi ndipo aganiza zopuma kaye mu ndale zachipani.

Ken Msonda People's Party Joyce Banda

Msonda: Atuluka PP.

“Ndakhala ojijilika pa ndale kuyambila 1994, tsopano ndikufuna ndipumulile kaye,” anatero a Msonda polengeza za chiganizochawo.

Koma a Msonda anatsindikanso kuti kutulukakwawo mu chipani cha Peoples’ sindiye kuti basi azitayilatu pansi ndale.

“Nditulukilanso, mu zisankhoza 2019 ndikupita kukaimila ku Rumphi East. Anthu a ku Rumphi musadandaule, ndilinanu,” anatero a Msonda.

Dera la Rumphi East padakali pano phungu wake ndi a Kamlepo Kalua amene ndimkulu wavuta ndiphokoso podzudzula boma la a Mutharika. Iyendiwa chiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha Peoples’.

A Msonda akhala mmodzi mwa anthu okhulupilika kuchipani cha Peoples’ anthu ambiri atachitaya kutsatilaku luzachitsankhokwachipanichindikuthawam’dzikomunokwamtsogoleriwachiapnichi.

Pa nthawi ina a Msonda anapeza mavuto atalangiza a Malawi kuti aphe anthu onse ochita mathanyula ati chifukwa Buku lopatulika limaletsa mchitidwe umenewu.75 Comments On "Msonda azitaya, atuluka PP"