Kasambara agamulidwa: akasewenze ya kalavula gaga kwa zaka khumi ndi zitatu

Advertisement
Ralph Kasambara

Bwalo la milandu lalikulu mu mzinda wa Lilongwe dzulo lachiwiri pa 30 August lalamula nduna yakale yoona za malamulo a Ralph Kasambara kuti akagwire ukaidi wa kalavula gagag kwa zaka khumbi ndi mphambu zitatu.

A Kasambara anapezeka olakwa pa mlandu okonza upo ofuna kupha a Paul Mphwiyo mu chaka cha 2013.

Malingana ndi oweruza mlandu wa bwaloli a Justice Micheal Mtambo, a Kasambara akuyenela kukasewenza kwa nthawi yochuluka chonchi kamba koti mlandu umene anapezeka olakwa ndi waukulu. Oweruza mlanduyu ananenanso kuti a Kasambara apatsidwa chilango chokhwima chonchi Kamba koti anaonetsa kusaweruzika mu nyengo imene amaimbidwa mlandu.

Ralph Kasambara
Kasambara (Pakati) amangidwa.

“Inu ndi munthu oipa mtima kwambiri,” oweruza mlandu anadzudzula choncho a Kasambara. “Nthawi yonse yomwe mumaimbidwa mlandu munaonetsa khalidwe ngati mbuli yosazindikila ngakhale muli munthu odziwa malamulo wamkulu.

“Inu munalankhula zinthu zoti sizimayenela kulankhulidwa mu bwalo la milandu ndipo munakhala mukuopseza anthu. Inu simunasonyeze chisoni kapena kuzichepetsa mu nthawi yonse yoimbidwa mlandu,” anatero Mtambo.

Oimira mlandu a Kasambara amapempha bwalo kuti liwamvele chisoni ndi kuwapatsa ka chilango kochepa ati poti a Kasambara ndi mkulu amene wathandiza dziko lino ngati mkulu wa za malamulo komanso nduna yaboma, iwo anaonjezelapo kunena kuti a Kasambara ndi munthu wa chichepele amene angathe kuthandiza dziko lino.

Zonse anakambazi sizinaphule kanthu pamene a bwalo analimbira mtima a Kasambara ndi kuwatumiza kundende kwa zilumika khumi ndi zitatu.

Ena amene anapezeka olakwa pamodzi ndi a Kasambara ndi a Pika Manondo ndi a MacDonald Kumwembe. Awiliwa awakwapula ndi zaka makumi awiri kuonjezerapo mphambu zisanu ndi imodzi aliyense pa mlandu ofuna kupha a Mphwiyo komanso okonza upo ofuna kupha a Mphwiyo.