Kasambara agamulidwa: akasewenze ya kalavula gaga kwa zaka khumi ndi zitatu

Advertisement
Ralph Kasambara

Bwalo la milandu lalikulu mu mzinda wa Lilongwe dzulo lachiwiri pa 30 August lalamula nduna yakale yoona za malamulo a Ralph Kasambara kuti akagwire ukaidi wa kalavula gagag kwa zaka khumbi ndi mphambu zitatu.

A Kasambara anapezeka olakwa pa mlandu okonza upo ofuna kupha a Paul Mphwiyo mu chaka cha 2013.

Malingana ndi oweruza mlandu wa bwaloli a Justice Micheal Mtambo, a Kasambara akuyenela kukasewenza kwa nthawi yochuluka chonchi kamba koti mlandu umene anapezeka olakwa ndi waukulu. Oweruza mlanduyu ananenanso kuti a Kasambara apatsidwa chilango chokhwima chonchi Kamba koti anaonetsa kusaweruzika mu nyengo imene amaimbidwa mlandu.

Ralph Kasambara
Kasambara (Pakati) amangidwa.

“Inu ndi munthu oipa mtima kwambiri,” oweruza mlandu anadzudzula choncho a Kasambara. “Nthawi yonse yomwe mumaimbidwa mlandu munaonetsa khalidwe ngati mbuli yosazindikila ngakhale muli munthu odziwa malamulo wamkulu.

“Inu munalankhula zinthu zoti sizimayenela kulankhulidwa mu bwalo la milandu ndipo munakhala mukuopseza anthu. Inu simunasonyeze chisoni kapena kuzichepetsa mu nthawi yonse yoimbidwa mlandu,” anatero Mtambo.

Oimira mlandu a Kasambara amapempha bwalo kuti liwamvele chisoni ndi kuwapatsa ka chilango kochepa ati poti a Kasambara ndi mkulu amene wathandiza dziko lino ngati mkulu wa za malamulo komanso nduna yaboma, iwo anaonjezelapo kunena kuti a Kasambara ndi munthu wa chichepele amene angathe kuthandiza dziko lino.

Zonse anakambazi sizinaphule kanthu pamene a bwalo analimbira mtima a Kasambara ndi kuwatumiza kundende kwa zilumika khumi ndi zitatu.

Ena amene anapezeka olakwa pamodzi ndi a Kasambara ndi a Pika Manondo ndi a MacDonald Kumwembe. Awiliwa awakwapula ndi zaka makumi awiri kuonjezerapo mphambu zisanu ndi imodzi aliyense pa mlandu ofuna kupha a Mphwiyo komanso okonza upo ofuna kupha a Mphwiyo.

 

Advertisement

68 Comments

  1. Hello my name is john I want to give a testimony about my HIV virus that was cured by a great spell caster. Since last 4years I have being a HIV AID patient. I never think I will live long again and am so grateful to Dr sule who help me cured my HIV AIDS last 3 weeks. I was in a great pain so I told one of my best friends; he told me that there is a great spell caster that can cure my VIRUS. I asked him if he had his contact, he gave me his contactl, I contacted him he talked to me and he perform the necessary things and sent it to me through corrier delivery company and deliverd to me at my place and he told me that after two weeks I should go for a test. Which I did, when the doctor told me that am now a HIV negative I couldn’t believe myself I went to see another doctor the result was still the same, I was human on planet earth, so I emailed him and thanked him. Please if you are having a similar problem please visit him/contact him via whatsapp +2348162447651

  2. #bambo kasambala* ndikufunilani kulavulagaga kwabwino ndagovakumene KUTI ng’ombezatembeka kuyana kudazibomo sindikuwakuti mmenezimatele masexchoni anu analikuto monga mkuluwama sexchoni eeeee APA zikungooneselatu KUTI paribe wapambana lamulo ndavomeleza kanene Ku Zambia nanutso tumakasamba tatin’gonotin’gono mutengelepo phuzilo the end went ,,,,,comment lodng tauch angen to sev

    1. Ndende ilibenso kut ukudya bwino..mayaz….as long as ali mu cage..bas…anva kuwawa…..kukhala pa wekha No!! Dona muthu wabanj its not a joke..

  3. Ndikuwafunila mafuno abwino bambo Kasambala kalimeni chimanga chokwanila. Mbatata. Masamba okwanila. Koma tikuonjezelani zaka tikafika mu December chaka chino.

  4. Kma sitikuziwa chifkwa chomwe akukalavurila gaga Ralph kambala#mwangoti akukaxenza kma tkufna mutiuze bwino lomwe coz tizapala utsi malo mopala moto tiuzeni…enafe stikuziwa

  5. Udolowo watha basi, akagwira ameneyo. Apanso m’mene kwateremu lero wayamba kulavula gaga. Anakafuna za udolo anakachita asanafike pamaso pa bwalo la jugde munzinda wa Lilongwe, bambo Kasambara gwirani bwino ntchito kumeneko limani chimanga chikufunika m’dziko muno.

    1. Kkkk usaiwale paja ika lembedwa nchizungu oika nde manga nchizungu sakwana 5 koma oika nde manga nchichewa amakwa 55

Comments are closed.