Juju! Wosewera wa FOMO, Dedza Dynamos akana kutuluka m’bwalo

Advertisement
TNM Super League

Okonda masewero a mpira wa miyendo anangoti kukamwa yasa Lamulungu pa bwalo la Mulanje Park pomwe wosewera wa FOMO FC ndi wina wa Premier Bet Dedza Dynamos anakana kutuluka m’bwalo la za masewero kupita kokapumulira mpaka onse kuonetsedwa makhadi ofiyira. 

Lamulungu pa 23 June 2024, timu ya FOMO FC inalandira pa bwalo la Mulanje Park timu ya Premier Bet Dedza Dynamos m’nchikho cha ligi yayikulu m’dziko muno ya TNM. 

Pomwe woyimbira masewerowa Cedric Mwachumu analiza khelele yake kuti ma timu awiriwa alowe m’bwalo kuti akachite majowajowa nkhondo yeniyeni isanayambike, anthu pabwaloli anadabwa kuona osewera ena ku ma timu awiriwa akukana kulowa m’bwaloli.

Mike Banda wosewera wa timu ya FOMO komanso Khumbo Banda wa timu ya Dedza Dynamos anakanitsitsa kulowa m’bwaloli kuti akatenge nawo mbali pa majowajowawo kamba koti aliyense amawumiriza mnzake kuti akhale oyamba kulowa m’bwalomo.

Pomwe anthu amawona ngati izi zinangochitika mwa ngozi, woyimbira atalizanso khelele kuthetsa chigawo choyamba, wosewera wa FOMO Oscar Mangwaya komanso wa Dedza Chifuniro Mpinganjira, nawo anakana kutuluka m’bwaloli kupita kokapumulira.

Izi zinakakamiza woyimbira masewerowa Mwachumu kuti awapatse osewera awiriwa aliyese khadi la chikasu, koma izi sizinaphule kanthu pomwe onse anakanitsitsabe kutuluka kamba koti aliyese amafunitsitsa kuti akhale omalizira kutuluka m’bwaloli.  

Zinatengera achitetezo kuwaduduluzira osewera awiriwa panja pa bwaloli ndipo woyimbira Mwachumu sanazengereze koma kutulutsa khadi lofiyira, kuti awiriwa asasewerenso masewerowa kamba ka khalidwe lolakwikali.

Pamapeto pa zonse, matimuwa anafanana mphamvu pomwe pa mphindi ya 90 Auther Mark Kalondola wa FOMO anabweza chigoli chomwe Samson Olatubosun anachinyira timu yake ya Dedza Dynamos kudzera pa penate. 

Masewerowa anathera 1-1 ndipo FOMO ili pa nambala 13 ndi mapoyitsi 11 pomwe Dedza Dynamos ili pa nambala 9 ndi mapoyitsi 12.

Advertisement

One Comment

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.