A Chilima akanika kutela pa bwalo la ndege la Mzuzu

Advertisement
Saulos Chilima

Ndege imene anakwera wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Klaus Chilima yalephera kutela pa bwalo la ndege la Mzuzu chifukwa cha nyengo yoyipa yomwe ili munzindawu.

Izi zakanikitsa a Chilima kukhala nawo pa mwambo woyika m’manda malemu Ralph Kasambara omwe ayikidwa mmanda tsiku la lero.

Malingana ndi malipoti, a Chilima amayenela kukhala nawo pa mwambowu womwe ukuchitikila m’mudzi mwa Chijere Chirwa m’boma la Nkhatabay.

Malipoti ena omwe tapeza akusonyeza kuti kulephera kwa Chilima kupezeka pa mwambowu ndi kamba koti akuyenera kukapezeka ku bwalo la ndege la Kamuzu munzinda wa Lilongwe pomwe mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera akuyenera kunyamuka kupita m’dziko la Bahamas.

Pakadali pano, talephera kumva kuchokera kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu chifukwa chokuti omuyankhulira wawo Pilirani Phiri sanayankhe lamya pa nthawi yomwe tinamuimbira.

Olemba: Mike Lyson Zgambo ndi Archangel Nzangaya

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.