Bungwe la MBS lati lipanga chipikisheni cha machesi osavomerezeka pa msika

Advertisement

Bungwe la Malawi Bureau of Standards (MBS) lati likhala likupanga chipikisheni mu misika komanso mawokala wonse m’dziko muno pofuna kuchotsa pa msika mitundu ya machesi omwe sanavomelezedwe ndi bungweli.

M’chikatala chomwe bungweli latulutsa  chati mitundu yina ya machesi monga Paka, Tinga, Kasuku , Mo komanso Soccer yomwe ikupezeka pa misika ya m’dziko muno siyili mukawundula wovomelezeka wa bungweli ngati chitsimikizo kuti mitundu  ya machesiyi ndiyoyenela kuti a Malawi atha kugwiritsa ntchito popanda vuto komanso kuyika miyoyo yawo pa chiwopsyezo chilichonse.

 Poyankhura m’chikatalachi ,Mkulu  wa Bungwe Dr Bernard Thole  wati  bungweli likupempha komanso kulangiza a Malawi ndi eni magolosale ndi mawokala ndi ena onse ochita malonda kuti asagule kapena kugwiritsa ntchito mitundu ya machesi  yatchulidwayi.

A Thole anawonjezera ponena kuti bungweli likulangiza komanso kuchenjeza onse opanga, kuyitanitsa komanso kugawa mitundu ya machesiyi kuti pali ndondomeko komanso milingo yomwe imayenera kuti itsatidwe popanga , kuyitanitsa komanso kugulitsa katundu ngati ameneyu pansi pa  ndondomeko ya chilolezo yomwe pa chingerezi amaitcha permit and Imports Quality Monitoring Schemes.

“Bungwe la MBS likulangiza onse omwe akupanga mabizinesi wosiyanasiyana oyitanitsa katundu kunja kulowa m’dziko muno kuti asanayitanitse kapena kubweletsa katundu wina aliyense, amayenela kubweletsa ku ma ofesi a MBS gawo lochepa lakatunduyo yemwe akafuna kuyitanitsa (pre-shipment sample) pa chingelezi.

“Izi zimathandizira kuti amuyeze kuti apeze chitsimikizo komanso chivomelezo choti atha kubweletsa katundu wawo m’dziko muno atawunikiridwa ndi a MBS pomuyeza pa makina ndipo kuti zotsatira zake zawonetsa kuti alibwinobwino malingana ndi milingo yadziko lino,” anatero powonjezera.

Mkulu wa bungweli watinso kudzera mu ndondomekoyi, bungweli limawonetsetsanso kuti katundu wosafikira milingo ya dziko lino yemwe angayike pa chiwopsyezo miyoyo ya anthu omugwiritsa ntchito komanso chilengedwe, asapeze danga lopezeka pa misika ya dziko lino.

Bungwe la MBS ndi bungwe la boma lomwe linakhazikitsidwa mu chaka cha 1972 ndi malamulo a dziko (Act of Parliament, Cap 51:02) ndipo anawunikiridwanso mu chaka cha 2012 (Revised Act No. 14 of 2012).

Bungwe la MBS lidapatsidwa mphamvu ndi udindo umenewo ngati njira imodzi yopititsira patsogolo nkhani za chuma chadziko lino, potukula ntchito zamalonda, powonetsetsa kuti katundu komanso malonda zikupangidwa molingana ndi milingo yadziko lino.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.