Masewero awiri, ma pointi awiri – mtunda wa ligi utha kutalika kwa Bullets

Advertisement
Big Bullets, Mighty Tigers draw

Kapena tiyambirenso ligi kapena, mwinatu ndi kubwela kwa Mzuzu City Hammers kapena. Ena a nyerere akuti ndi kusowa kwa ma penalty. Koma amene akuteteza chikho cha TNM Super League zikuoneka kuti sizinawayambire bwino ndithu.

Atalepherana ndi timu ya Dedza Dynamos sabata latha mu masewero awo oyamba a ligi, timu ya Bullets yakanikananso ndi timu ya Tigers lero pakwawo pomwe pa Kamuzu stadium.

Pa masewero amene Bullets imayembekezereka kuti ipambane kuti itsimikizire owatsatira kuti iyo idakalimo, timuyi yakanika kupereka uthengawu.

Anali masewero opereka chidwi pomwe otsatira Bullets anakhamukira ku bwalo la Kamuzu kuti akamwe wamkaka, koma pamapeto pa zonse a Bullets sanapaone pagolo ndipo nawo a Tigers sanapaonenso.

Kusachita bwino kwa Bullets kutha kupereka phuma ku maneba awo a Mighty Wanderers amene mawa lino akhale akusadzulana ndi FOMO ya ku Mulanje. A Wanderers Sabata latha nawo analepherana ndi Tigers yomweyi 1 kwa 1 zimene zidapangitsa mphunzitsi wawo kunena kuti anyamata ake adali ndi phuma.

Advertisement