Bukhu loyera Mateyu 22 vesi la 21 Akhristu ambiri akulidziwa ndipo akuyenela kuchita umo linenela.
M’busa otchuka mu mzinda wa Blantyre, a Joseph Ziba amangidwa ati kamba kothawa kupeleka msonkho okwana 26 miliyoni Kwacha.
Malinga ndi malipoti, a Ziba anagula galimoto lapamwamba kwa mmwenye wina Tayub Aziz imene inali yosalipilidwa msonkho.
Bungwe la misonkho litapeza a Ziba kuti alipile msonkho wa 26 miliyoni pa galimotoyo, ati iwo koyamba anavomela.
Koma kenako anachita ukambelembele ndi kupita ku khoti kukatenga chiletso kuti a bungwe la msonkho asawalande galimoto kapena kuwakakamiza kulipila.
Atazindikila za njomba yomwe munthu wa Chautayu anachita, a bungwe la misonkho nawo anapita kukhoti komweko kukapempha kuti achotse chiletso chija. Izi zinatheka.
Ndipo akuti dzulo Apolisi pamodzi ndi a bungwe la misonkho ananjata abusa a Ziba pamodzi ndi mzawo anawagulitsa galimotoyo.
This is what we call Bad or Wrong reporting. If this is what we would expect from journalist, then it is only right to change jobs.
God knows
Abusa ngati zili choncho ayi munalakwitsa chifukwa satana salimbana ndi anthu ake amalimbana ndi ana a Yehova chonchonso munthu wamulungu akalakwitsa nkhani imathamanga kwambiri than yamunthu osakhulupirira komabe sibwino kuti tikuweluzeni chifukwa nthawi zina anthu antha kunena zambiri koma chilungamo chake mukuchidziwa ndiinu ndi Yehova wanu chilungamo chioneka.Yehova akuthandizeni munyengo yowawitsayi
A M R A Mulungu Akukanthani Simungamange Man Of God!
Nkhani yi sikumveka bwino.
Shame on you Ziba.
mukuyitsata bwino nkhaniyi? kapena mungobwetuka?
ineso kudabwatu
zachamba basi tamaleni zoveka bwino kale mumati wamangidwa chifukwa galimoto yake sanasonkhele msonkho
If you dont know the case, please close your toilet and wait
Ali police iti ndwapitisire nsima?
Ukundisekesa bwanji ndipo iwe ndi munthu wabodza ndithu ali kuno ku police ya honeydew
olo abodza muchuluke…..pastor ziba no reverse kupitabe chitsogolo
Bodza mwachedwa munali kuti awatulusa pa bell
Follow
Admin shut up. If You dont know what you are posting . Seems you dont know the real side of the story
galimotoyo inagulidwa pa ntengo wabwani
ubwino wake wanena akhristu osati asilamu kut akulidziwa ndiye ife zisatikhuze zanuzo athana nazo okha
Nawe tazingodikilira tsiku lolandila mitu ya mbuzi mmipanda mwa amwenyemu, ngati sizikukhuza ukulowelera bwanji? Pita ukapempherere amwenyemu akupatse 200 kugulitsa pemphero
Kkkkkkk kma man mpaka mitu yambuzi kkkk
musova man simunati or chopeleka mupeleka ndi abakha omwe koma sizikwanira pa figure yomwe akufuna a custom m ‘ busa wanji othawa misokho
Fake news