Oganizilidwa pa milandu yakupha adzitengeledwa ku khothi mwansanga – Kaiyatsa

Advertisement
Kaiyatsa

Mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), Michael Kaiyatsa wapempha anthu m’dziko muno kuti apewe m’chitidwe ophana ponena kuti aliyense ali ndi ufulu okhala ndi moyo.

Kaiyatsa wanena izi kutsatira kukula kwa chiwerengero cha imfa zodza kamba kophedwa, pomwe posachedwapa apolisi ku Mponera m’boma la Dowa amanga bambo wazaka 31 zakubadwa a Luke James kamba kopha mzake atasemphana maganizo pa nkhani yokhudzana ndi masewero a mpira wa miyendo.

Malinga ndi Kaiyatsa, ndi zodandaulitsa kuti anthu akupitilirabe kuphana angakhale kuti malamulo adziko lino amateteza bwino mwapadera ufulu okhala ndi moyo komanso kutsindika momveka bwino zokhudza ufuluwu ponena kuti palibe uyo ali ndi ufulu opha munthu mzake.

Iye wati mkofunika kuti anthu aphunzitsidwe bwino zokhudza ufulu okhala ndi moyo komanso akuyenera azindikire zokhudza ufulu umenewu.

Iye watinso ndi kofunika kuti mabwalo a milandu athandizepo pa nkhani ngati zimenezi kuti zikachitika okhudzidwa azitengeledwa ku bwalo la milandu mwansanga kuti akazengedwe mulandu, ndipo akapezeka olakwa apatsidwe chilango chokhwima.

Kaiyatsa wati ndi zodandautsa kuti pakadali pano kumabwalo amilandu kuli milandu yambirimbiri yomwe sidathe yokhudzana ndi kuphana ndipo iye wati izi ndizodandaulitsa kaamba koti izi zili ndi kuthekera kokolezera mchitidwewu.

Malinga ndi Kaiyatsa, ina mwamilanduyi ndi monga kuphana kamba koganizirana ufiti, kupha anthu omwe akuganizilidwa kuti apalamula milandu, komanso milandu yokhudza kuphana anthu akayambana.

Apa iwo ati ndikofunika kuti malamulo agwire ntchito ndicholinga choti mchitidwe umenewu uchepe mdziko muno.

Advertisement