Letsani mitala ndipo pasapezeke obeleka ana oposa awiri – Phungu auza boma

Advertisement
Maize scandal

Phungu wa dera la kumadzulo mu boma la Nsanje, a Chidanti Malunga auza Boma kuti likhazikitse lamulo loletsa a Malawi kubeleka ana oposa awiri.

dr-joseph-chidanti-malunga
Chidanti Malunga: Anthu asamakhale ndi ana oposa awiri

A Malunga anauza wailesi youlutsa mawu ya boma ya MBC kuti boma likuyenela kuchitapo kanthu kuti achepetse chiwelengelo cha anthu mu dziko muno.

“Anthutu tikuswana ndipo ngati sitichenjela, tikhala pa mavuto adzaoneni,” anatelo a Malunga.

Iwo ananena kuti pofuna kupewa mavuto amene angadze ngati a Malawi angapitilize kuswana ngati ngumbi, Boma likuyenela kukhazikitsa lamulo loletsa anthu kukhala ndi ana ambiri.

“Tikati banja lizikhala ndi mwana m’modzi basi ndiye ilakwa, a Malawi ambiri savomela. Koma tinene awiri, anthu asamakhale ndi ana oposa awiri,” anatelo a Malunga.

Iwo anaonjezelapo kuti Boma lionjezelepo poletsa mitala.

“Mamuna azikhala ndi mkazi m’modzi basi. Osati uku mkazi wina kukabeleka ana kumeneko, uku wina kukabelekako ana,” anatelo a Malunga.