
Awa ndi malo otchedwa Chisangalalo kwa Manase mu mzinda wa Blantyre kumene madera ozungulira malowa monga Sunnyside, Manyowe, Nancholi, Naperi komaso Baluti amadalira kuti agule Makala.
Pa malowa, chaka ndi chaka pamakhala makala osakata ndipo nthawi zonse matumba amene amakhala ndi chimune ngati tsuko otchedwa “dumu” amakhala ali mbwe pamalopa.
Malawi 24 itacheza ndi modzi wa anthu ogulitsa makala amene amakatenga ku Nchalo m’boma la Chikwawa wanenetsa kuti amalipira binyira kwa ogwira ntchito yoteteza nkhalango ku unduwa wa za nkhalango amene amakhala mu mseu wa Chikwawa.
Pa thumba lilinso, iye wati amapereka ndalama yokwana K7,000 kuti adutse nalo kuchokera ku Chikwawa kufika kwa Manase.
Atafunsidwa za zikalata zodziyenereza kuchita malondawa ndi cholinga chopewa kulipira kwa amaliwongowa, iye wati anthu ogwira ntchitowa sangalore kuti iwowa azigwiritsa ntchito izi kamba koti amadandaula kuti amapilidwa ndalama zochepa kotero amadalira banyira amene anyamatawa amawapatsa.
Dziko lino lakhala lili pa mavuto osowa chakudya chokwanira kwa zaka tsopano ndipo zonsezi zikudza kamba ka kusintha kwa nyengo komwe gwero lake ndi kuononga chilengwedwe mwachisawawa.
Koma chomvetsa chisoni adindo oteteza chilengwedwe ndi ameneso ali pa tsogolo kukolezera tchitidwe osakaza chilengedwe.
Ndiye anthu wamba alowera kuti ?
Dziko lino likufunikira zintchito za nduna Vitumbiko Mumba zitafikira maunduna onse m’dziko muno.