Ngati mbali imodzi yotukula achinyamata pa chuma m’dziko muno, mabungwe a Malawi Congress of Trade unions (MCTU) komanso Employers’ Consultative Association of Malawi (ECAM) ati akonza ndondomeko yophunzitsa achinyamata 800 kupeza luso la ntchito za magetsi ogwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa.
Mkulu owona za ntchitoyi ku bungwe la MCTU, a Joseph Kankhwangwa, ati ntchito za luso, makamaka zokhudza magetsi ogwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa zili ndi kuthekera kokweza chuma cha dziko lino.
A Kankhwangwa anena izi pa sukulu yophunzitsa ntchito za luso la manja ya Khwisa m’boma la Balaka pamene amafotokozera mafumu, adindo osiyanasiyana komanso ophunzira za pulojekitiyi.
Malingana ndi a Kankhwangwa, sukulu ya Khwisa ndi imodzi mwa sukulu zosula luso m’dziko muno zomwe zipindule mu ndondomekoyi.
“Mu gawo loyamba lomwe liyambe pa 6 January, 2025, ophunzira okwana makumi asanu (50) ndi omwe apindule mu maphunzirowa.
“Ngati MCTU, tidzapereka thandizo la ndalama komanso zinthu zina zowathandizira achinyamatawa mu maphunziro awo,” anatero a Kankhwangwa.
Iwo adaonjezera kunena kuti oyenera kupindula mu purojekitiyi ndi achinyamata a zaka za pakati pa 16 mpaka 35.
M’mawu ake, mkulu oyang’anira sukulu ya Khwisa, a Mavuto Mtitimila, anati pulojekitiyi yabwera pa nthawi yake ndipo ithandizira ana ambiri maka iwo ochokera m’mabanja osowa kupeza luso komanso kutuluka miyoyo yawo.
Wapampando wa khonsolo ya Balaka, khansala Pharaoh Kambiri adayamikira mabungwe a MCTU komanso ECAM pobweletsa maphunzirowa m’boma la Balaka ponena kuti ithandizira achinyamata kupeza chochita.
Purojekiti ya Zantchito ndi ya zaka ziwiri ndipo ikugwilidwa ndi thandizo la ndalama kuchokera ku mgwirizano wa maiko aku ulaya (European Union).