Nafe tazitaya: PP yatuluka mu mgwirizano wa Tonse

Advertisement
Peoples Party

Pamene masiku akupitilirabe kuthera kuchitseko kuti dziko lino lipangitse chisankho chapatatu chaka cha mawa chomwe chidzasankhe Mtsogoleri wa dziko, Aphungu a ku Nyumba ya Malamulo komanso ma Khansala, chipani cha People’s (PP) chalengeza kuti sichilinso mu m’gwirizano wa Tonse.

A Joyce Banda ayankhula izi ku Naisi m’boma la Zomba komwe chipani cha PP chinachititsa msonkhano ngati njira imodzi yokonzekera zisankho za chaka cha m’mawa.

Iwo ati; “Sikuti lero tabwera kudzatuluka Tonse Alliance, koma anatiuza kuti pokalowa ku konveshoni yawo (mgwirizano) wathera pomwepo. Kodi konveshoni apanga kapena sanapange? Ndiye posafuna kungomvera za m’maluwa ndinanyamuka kupita kumpoto kukaonana ndi apulezidenti.

“Ndimati ndikuuzeni kuti ife tiyenda tokha iwoso anavomera kuti nawoso ayenda okha; koma momwe zikuonekera palibe yemwe akafike kumapetoko ndi 50+ tikadzionera konko. Kumeneko ndi komwe anthu adzikafunana.”

A Banda omwe anakhalapo mtsogoleri wa dziko lino kwa zaka ziwiri potsatira imfa ya malemu Bingu wa Mutharika mu 2012, ati kuyambira pano akhala akulimbikitsa chipani chawo kuti chizachite bwino pa zisankho za 2025.

Chipani cha PP ndichachinayi kutuluka mu mgwirizanowu omwe udapangidwa ndi cholinga chofuna kugwetsa boma la a Peter Mutharika pomwe khothi lalikulu m’dziko muno lidalamura kuti pakhalenso chisankho chachibwereza chofuna kusankha mtsogoleri wa dziko lino kamba kakuti chisankho chomwe chidachitika mu chaka cha 2019 chidali ndi zolakwika zambiri.

Oyamba kutuluka mu mgwirizanowu adali a Kamuzu Chiwambo a Petra ndipo a Yeremiah Chihana a Aford anatsatira pambuyo pake.

Chipani cha UTM, chomwe mtsogoleri wake a Saulos Chilima adamwalira pa ngozi ya ndege pa 10 June mu nkhalangoya Chikangawa, chidatulukanso mu mgwirizanowu ndipo PP ndi yomwenso lero yalengeza kuti zathapo.

Advertisement