Mapulasitiku apume: Makondomu ayamba kupezeka ku Likoma

Advertisement
Likoma Island

Anthu pa zilumba za Likoma ndi Chizumulu atha kuusa moyo tsopano kamba koti atatha masabata angapo akugwiritsira ntchito mapulasitiki pogonana, ofesi ya zaumoyo pa zilumbazi yalandira makondomu.

Mkulu wopititsa patsogolo nkhani za umoyo m’boma la Likoma, Jomo Sumani watsimikizira nyumba zina zofalitsa nkhani m’dziko muno kuti ofesi ya zaumoyo yalandira makatoni asanu momwe muli makondomu okwana 26,000 kuchokera kupolisi ya Likoma.

Pothokoza a Sumani ati, “Thandizo la makondomu lomwe a polisi atipatsa lithandiza kwambiri pa ntchito yolimbana ndi matenda opatsirana pogonana kuphatikizapo HIV/AIDS m’boma lino.”

Mkulu wa polisi ku Likoma, Spencer Jinja wati thandizoli lachokera kwa Emma Ngosi wochokera ku likulu la polisi ya Marine ku Monkey-Bay kudzera mu gwirizano ndi Pakachere Institute for Health Communication and Development.

Thandizoli ladza pomwe sabata yatha zinadziwika kuti anthu m’bomali akhala akugwiritsa ntchito mapulasitiki kulowa m’malo mwa makondomu omwe akhala asakupezeka kwa ka nthawi zomwe zimayika miyoyo ya anthu ochuluka pa chiopsyezo chotenga kapena kupatsirana matenda opatsirana pogonana.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.