Wanjatidwa kamba kopezeka ndi mankhwala popanda chilolezo

Advertisement
Malawi24

Apolisi m’boma la Salima, amanga bambo wina wazaka 31 zakubadwa yemwe dzina lake ndi Mathews Daimon, kamba komuganizira kuti amasunga mankhwala achipatala osiyanasiyana popanda chilolezo mnyumba mwake.

M’neneli wa apolisi m’bomali, Sub Inspector Rabecca Ndiwate, watsimikiza za nkhaniyi ndipo iye wati iwo amanga bamboyu kutsatira kutsinidwa khutu ndi anthu ena akufuna kwabwino ponena kuti bamboyu amasungira mankhwala amitundu yosiyanasiyana.

Apolisi atamva zankhaniyi, sanachedwe koma kuthamangira kunyumba ya mkuluyu komwe anakachita kafukufuku ndikukwanitsa kupeza mankhwala osiyanasiyana monga indosidi, amokisilini, dikolofenake ndi ena ambiri.

Bamboyu atafunsidwa kuti apereke chilolezo chomuloleza kukhala ndi mankhwala amenewa, iye analephera kutero.

Apa polisiwa sanachedwe koma kumanga bamboyu ndikukamusunga mchitokosi cha apolisi.

Daimon amachokera m’mudzi mwa Moya kwa Mfumu yayikulu Karonga m’boma la Salima ndipo posachedwapa akaonekera kubwalo la milandu komwe akayankhe pa mulanduwu.

Advertisement