Anthu 24 omwe anagwira Njakata afika kwawo

Advertisement
Yeremiah Chihana

Anthu okwana 24 ochokera m’boma la Mchinji omwe anagwira njakata masiku apitawa pamene Phungu wa nyumba ya malamulo wa dera la ku mpoto m’boma la Mzimba a Yeremiah Chihana atawagwiritsa ntchito ku famu yake koma kukanika kuwalipira malipilo malingana ndi m’gwirizano wawo tsopano anthuwa afika  kwawo ku Mchinji.

Anthu akufuna kwabwino ndi omwe anazipereka pothandiza ndi magalimoto komanso mafuta.

Anthuwa anakhala masiku awiri pa ofesi ya za ntchito ya boma la Mzimba atayenda mtunda wa makilomita 80 kuchokera ku Geza Mbalachanda komwe amagwira ntchito zakumunda.

Mkulu wowona zachisamaliro cha wanthu ku nkhonsolo ya m’bomali makamaka chigawo cha kumwera a Bernard Nangwele wayamikira anthu wonse womwe anategapo gawo powonetsetsa kuti anthuwa akafika kwawo.

Wapampando wa mabungwe omwe asali a boma ku Mzimba Christopher Melele wati pakali pano amuyitanitsa phunguyi ndicholinga chakuti anthu 24 wa apeze chilungamo, Melele watinso phunguyi akapanda kufika ndiye kuti amutengera ku bwalo la milandu.

“Ife ngati amabungwe tikufuna chilungamo chioneke pa anthu awa, ndizomvetsa chisoni kuti munthu yemwe akupanga malamulo ndi amenenso akutsogolera kuphwanyaso malamulowo, timuitanitsa phunguyi akakanika kufika timutengera ku khoti,” watero Melele.

Poyankhulapo pa nkhaniyi,  Yeremiah Chihana wati iye ndiwokonzeka kukumana ndi amabungwewa.

“Ndilibe vuto ine kukumana ndi amabungwewa ndipo ndili okonzeka, ndikudziwa kuti ndikakumana nawo akamvetsa bwino zazomwe zinachitika”. Watero Yeremiah poyankhula ndi Malawi24.

M’modzi mwa a phungu a m’boma la Mchinji Godfrey Kapalamula wathokoza anthu onse omwe anatengapo mbali pothandiza kuti anthu akudera la kwawo afike bwino.

“M’malo mwa anzanga onse ndithokoze anthu aku Mzimba pa ntchito yomwe ayigwira, mwachita zinthu zapamwamba pothandiza abale athu womwe anagwira njakata, mwasonyeza u Malawi weni weni,” Watero Kapalamula .

Anthu ambiri akupitiliza kudzuzula a Chihanaposalabadilra anthu womwe anali kuwagwilira ntchito.