Mphungu wa nyumba yamalamulo ku dera lapakati m’boma la Ntcheu, Norman Chisale wati anthu ayiwale zoti adzagwetsedwa pa mpandowu ndipo wanenetsa kuti adzachita kusiya yekha akadzafuna.
Poyankhula ndi imodzi mwanyumba zofalitsa nkhani mdziko muno, Chisale wati amathandiza anthu a dera lake, kufika pomapereka malipiro ake apamwezi kuti anthuwa adzigwiritsa ntchito pa zachitukuko.
“Ndiku tchalenja kuti ndikadzafuna ndidzasiya ndekha udindo wanga ngati phungu wa dera lino, koma kugwetsedwa ine ndie ayi. Ngakhale malipirp anga sindilandira, amatenga okha ku derako kumagwiritsa ntchito” anatero Chisale.
Phunguyu amayankha, atafusidwa za mau omwe anayankhula pa msonkhano wina ku dera lake kuti otsatira chipani cha UTM adzipatsidwa makofi.
Chisale wati mau amenewa anawayankhula ndi mkwiyo ndipo ankapita kwa munthu wina wa UTM waku dera lakelo, yemwe ankamuyipitsira mbiri.
“Mau amene aja sindinkhanena onse a UTM ndipo UTM ndilibe nayo udani, koma munthu wina oganiza ngati mphemvu yemwe anakasuma kuti ndinabera chisankho komaso ndinkapereka ndalama kwa anthu pa nthawi yokopa anthu, zomwe zinali zabodza”
Wachiwiri kwa nduna ya chitetezo cha mdzikoyu wati wakhala akuthandiza anthu a dera ake kuchokera nthawi ya UDF ndipo sangasiye kamba koti munthu wina sakukondwera nazo.
Chisale anamaliza ndikutsindika kuti atafuna kupuma ngati phungu, munthu olowa mmalo make alipo kale, ndipo anati ndi Kauwa yemwe wati amakhala bwino ndi anthu komaso ndi wodzichepetsa.