Ndale zikusokoneza ubale wa m’tsogoleri wa dziko ndi wachiwiri wake – PAC


President Arthur Peter Mutharika with Vice President Jane Ansah

Bungwe la Public Affairs Committee (PAC) lati kusagwirizana pakati pa mtsogoleri wa dziko lino ndi wa chiwiri wake, ndichitsimikizo choti m’dziko muno ndale ndizomwe zimagwira ntchito kwambiri kuposa malamulo.

Izi ndi malingana ndi woyankhulira bungwe la PAC a Bishop Gilford Matonga omwe anena izi Loweruka pomwe amayankhula ndi imodzi mwa nyumba zowulutsa mawu mdziko muno.

A Matonga ati kusagwirizana komwe kukuoneka pakati pa Peter Mutharika komanso wachiwiri wake Jane Ansah, ndi kaamba koti ndale zikugwiritsidwa ntchito kwambiri kuposa lamulo.

Iwo ati malingana ndi malamulo, wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko amayenera adzipatsidwa ntchito zoti agwire, zomwe wati pano sizikuchitika pazifukwa za ndale.

Gilford Matonga- Malawi24
Matonga: Ndale zikuposa lamulo

“Udindo wa Vice President uli mu constitution ya Malawi ndipo uli ndi zinthu zoyenereza kuti udindowo ugwire bwino ntchito ndipo ngati dziko tinayenera kulemekeza constitution ya Malawi,” watero Matonga.

Matonga watiso malamulo a dziko la Malawi mbali zina sadathandize chifukwa adapereka kusiyana pakachitidwe ka zinthu zina zokhudzana mipando iwiriyi.

Iwo ati pali kuthekera kwina kumene kudapelekedwa kuti wachiwiri kwa m’tsogoleri akhoza kusankha kuti asanvele bwana wake ndipo bwanayo sangapange chilichonse chotsutsa ganizo la mbali inayo.

“Malamulo athu sanatithandize mbali zina pa nkhani za mipando iwiriyi, chifukwa nthawi zina Vice President akhoza kuganiza kuti asanvele bwana wake, ndipo bwana wakeyo sangachite chinthu chilichonse,” wateroso Matonga.

Latest vacancies

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading