Madobadobawa simudzawawonaso – Chisale


Normanchisalejpg- Malawi24
Nanga angalime? Ayitu, madobadobawo ntchito ndiyomweyo. Komabe, kuyambira lero lolemba akuyenera kupeza dimba poti nduna yanenetsa kuti iwaonetsa chidameta nkhanga mpala.

Wachiwiri kwa nduna yachitetezo mdziko, Norman Chisale walengeza kuti kuyambira lero lolemba, madobadoba omwe amapezeka ku maofesi a nthambi yopanga ziphaso zoyendera sadzapezekaso.

Poyankhula loweruka, Chisale wati ena mwa mavuto omwe anthu akukumana nawo akamakozetsa ziphaso zoyendera, akudza chifukwa chamadobadoba.

“Ndilengeze lero kuti kuyambira lolemba sikukhalaso ma dobadoba chifukwa akubweretsa mavuto,” watero Chisale.

Chisale wati malo opangitsira ziphaso amayenera kukhala a anthu olembedwa ntchito ndi boma okha, ndipo wati oyenera kuthandizidwa amayenera kukhala mwini chiphasocho.

Iye walengezaso kuti mchitidwe wa anthu omwe ali kunja kwa dziko lino omatuma achibale awo kukawapangitsira ziphaso wathetsedwa pano.

Ndunayi yadzudzula ulamuliro wa MCP posintha kampani yomwe inkapanga ziphaso zoyendera, ponena kuti yomwe anayitenga inkapanga ziphaso zochepa pa chaka.

Chisale wati anthu awapatse miyezi iwiri yokha kuti zinthu zilongosokepa nkhani yopanga ziphaso.

Latest vacancies

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading