Ndinakaba pakhomo pakwawo? – Chisale


Norman Chisale

Wachiwiri kwa nduna yazachitetezo cha mdziko, Norman Chisale wawuza anthu omwe amanena kuti ndalama zake ndizakuba, kuti nawoso akabe ndie akathandizire anthu ovutika.

Chisale wati ndizomvetsa chisoni kuti anthu omwe amalimbirikira kutukwanawa akawagwira amakhala otuwa, akumudzi ndipo zimadabwitsa kuti akuwatuma ndi ndani.

Poyankhula ndi Kanema wa Luntha, ndunayi inayankhula izi poyankha fuso lokhudzana ndi umoyo komaso thanzi la mtsogoleri wa dziko lino Arthur Peter Mutharika.

“Mtsogoleri akangotuluka pamapita ndalama zambiri ndie APM anangoti bola adzikhqla mu ofesi” anatero Chisale yemweso anapitiriza kuyankha fuso lakuti akamakhala mu ofesi samakhala akudwa “A Malawi Mulungu adzatilanga, zoti akudwala zinayamba 2012, koma mmene amatsika ndege ulendo uno sanachite manyazi?”

Iwo anatiso dziko lino ndipovuta kutukuka kamba koti anthu amakhalira mabodza ndi ugogodi.

“Mmene amamunyozera APM ndichimodzimodziso ineyo. Olo mmene ndimabwera kunoku ena amatukwana kuti ndalama zakuba, ndinakaba pakhomo pawo? Ngati zili zakuba nawoso akabe, akathandizire anthu ena tiwone ngati zingatheke”

Phungu wa dera lapakati m’boma la Ntcheu yu anati kuthandiza ndi mtima wa munthu osati kuchuluka kwa ndalama ndipo anatsimikiza kuti sadzasiya kuthandiza.

Latest vacancies

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading