Mneneri waomba mgolo: Chisale wakana kuvala nsapota za Mutharika


Images6- Malawi24

….komabe, wati mwina mu nthawi yoyikika zidzatheka

Uneneri wa mtumiki Thinos Kamanja ukuwoneka kuti kwapano waomba mgolo pomwe Norman Chisale watemetsa nkhwangwa pa mwala kuti alibe maganizo olowa m’malo mwa Peter Mutharika ngati mtsogoleri wa chipani cha DPP mu 2030.

Masiku apitawo, mneneri Kamanja ananenera kuti Mulungu wamuwonetsera kuti Chisale ndi yemwe akhale mtsogoleri wa chipani cha DPP kusinthana ndi Mutharika.

Koma Chisale yemwe ndi wachiwiri kwa nduna ya zachitetezo m’dziko komaso wachitetezo wa a Mutharika, wakana uneneriwu ponena kuti alibe lingaliro lotenga utsogoleri wa chipanichi.

Iye wati nthawi yomwe a Mutharika adzidzapuma pa ntchito mu 2030, iye adzatsagana nawo ku Mangochi kukapitiriza ntchito yake yowateteza.

Chisale wanenetsa kuti imfa yokha ndiyomwe idzamusiyanitse ndi mtsogoleri wa dziko linoyu.

“Chilichonse amalemba ndi Mulungu, mbiri yanga ndiyausilikali. Sindinkadziwa kuti ndidzakhala phingu wa nyumba yamalamulo kapena mtetezi wa a tsogoleri, ndiye zonse amapanga ndi Mulungu,” watero Chisale.

Iye wachenjeza kuti kutsogolera dziko sichinthu chamasewera choti aliyese angangodzuka ndikumanena kuti atsogolera dziko.

Atafusidwa chomwe adzachite ngati pempho loti atsogolere dziko litachuluka, iwo ati sadzalolabe kusintha ntchito yoteteza a Mutharika, ndipo ati mwina ganizo limeneli lidzakwaniritsidwa kutsogolo.

Latest vacancies

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading