
Patangodutsa masiku ochepa abusa a Church of Central Africa Presbyterian (CCAP) Blantyre Synod atayendera mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika kenako ndi kuyitanidwa kuti apalamula, nawo abusa oposa 50 a Nkhoma Synod ayendera ndi kupemphera ndi mtsogoleri wakaleyu ku nyumba kwawo ku Mangochi lero.
Pa mapempherowa a Mutharika anati iwo amakhulupilira mphamvu ya pemphero ponena kuti iwo ndi m’khristu ndithu komanso wa mpingowu, ndipo kuletsa kapena kutsekereza ena kuti asawayendere kupemphera nawo ndi kulakwa kwambiri.
Iwo ati Synod ina ikufunsa mafunso abusa omwe anafika kunyumba ya PAGE kudzapemphera nawo, apo ndi pomwe ati kutero n’kulakwa poti dzikoli likufunika kugwirana manja pakati pa azipembedzo ndi a ndale, chifukwa maguru awiriwa amafuna kuti moyo wa munthu uyende bwino.
Abusa a Chilumpha a ku Namitete CCAP mu uthenga wawo anati Malawi akuvutika ndipo Malawi akudikira a Mutharika omwe ndi munthu olimba mtima, pomwe anati mutu wa uthenga wawo ndi “Kuchilitsidwa kwa dziko lathu.”
Mtsogoleri wa abusawa a Chifunilo Damalankhunda anati abusa anali okondwa atamva kuti a Mutharika avomera kuti atsogolelenso dziko la Malawi.
A Damalankhunda anati abusa omwe amayenera abwere ku PAGE anali oposa 90 koma ena anabwelera m’mbuyo chifukwa cha mantha ndipo abwerawo ndi olimba mtima chabe, pomwe ati akuyembekezera kuti ulendowu ukhonzanso kubala dzisamani.
“Pompano mumva kuti eee … atengeledwera ku bwalo la milandu koma ife sitikatsekedwa pakamwa, mawondo kugwada kuti tikupemphereleni, ifeyo tikukupemphelerani,” anatelo a Damalankhunda.
Iwo anati akukhulupilira kuti a Mutharika akhale akuchita zinthu zabwino chifukwa cha ukadaulo wawo ndipo ati iwo ali nawo limodzi kuwathandiza.
Abusawa omwe anabwera limodzi ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi m’chigawo cha pakati a Alfred Gangata nawo anati Mulungu anawawonetsa abusawa kuti poyamba anathandiza m’busa mzawo poyesa ndi nkhosa koma qli Fisi, ndipo ati abusawa si okondwa ndi mmene zinthu zilili pano.
Posachedwapa abusa ena a mpingo omwewu wa CCAP koma mu Synod ya Blantyre anasumilidwa ku komiti yosungitsa mwambo chifukwa chopita kukayendera a Mutharika, komanso chifukwa chokuwa kuti DPP woyee! Pa nthawi ya mapempheroyo.
Abusa ozengedwawa anakana milandu yonse yomwe komiti imawayimba, ndipo wapam’pando wa komiti yosungitsa mwamboyi abusa a Joseph Thipa anatsimikiza pomwe anati zotsatira za bwaloli zituluka m’masiku akudzawa.