Mfumu imangiliridwa ku mtengo

Advertisement
Chief Juma

Tsoka likalimba amakulumadi ndi galu wako yemwe, ku m’mawa-ku adzukulu am’mudzi wa Maula, m’boma la Mchinji, T/A Ndawambe, amangilira kumtengo mfumu yawo a Juma kaamba koti asokoneza ndalama zachipepeso zomwe zimayenera kupita kwa anamfedwa.

Malingana ndi yemwe watiuza nkhaniyi ndipo ali kumwamboko, pali chikhulupiliro kuti mfumu Juma ndalamazi yasewelera njuga ya mtundu wa Aviator yomwe imachitika kudzera pa lamya za m’manja.

Aviator ndi ka ndege komwe kamauluka mothamanga, mochititsa jenkha ndipo kalibe nazo kuti ndalama wayika munthuyi ndiyachipepeso chaku maliro, afuna akokere.

Zateremu amfumuwa akuyenera kukhala omangidwa mpaka mwambo wamaliro uthe, mapeto ake pamakhala mwambo oti apereke chindapusa.