
Timu ya Bangwe All Stars yomwe yangotuluka kumene mu ligi yayikulu ya m’dziko lino ya 2024 TNM super, tsopano yathetsedwa chifukwa cha mavuto a zachuma.
Malinga ndi mwiniwake wa timu ya Bangwe, a Mphatso Jika wati malinga ndi kusowa kwa ndalama, kukhala kovuta kuti akwanitse kupitiliza kuthandiza timuyi pamene idzisewela mu masewelo a mu zigawo tsopano kufuna kudziguliranso malo mu ligi yayikulu.
Iye wati osewela akewa tsopano akhonza kuyamba kusaka ma timu omwe angakhonze kusewelera.
A Jika awuza nyumba zina zofalitsa nkhani kuti ndalama za osewela ku timuyi zimayambira 150,000 kukafika 400,000 ngat Malipilo ochepetsetsa ndi okwera kwambiri. Ndipo wati mwachitsamzo, osewela mu TNM Super League unkafuna ndalama zambiri monga 6 million Kwacha yomwe imafunika mu ulendo umodzi okasewera masewelo ku mpoto.
Timu ya Bangwe yomwe inalowa mu ligi mchaka cha 2023, idatuluka itagonja 4-1 masewelo ake otsiliza ndi Creck Sporting, chigoli chake chomaliza mchomwe adagoletsa ndi Patrick Phiri.
Bangwe yomwe inali imodzi mwa ma timu a mu mzinda wa Blantyre idatuluka itathera pa nambala 15 ndi ma points ake 27, ndipo idapakira limodzi ndi FOMO yomwe inamaliza ndi ma points 29 komanso Baka City ndi ma points ake 13 mchikwama kumalowera ku mpoto
Ena mwa ma timu pomwe anatha ochokera mu mzinda wa Blantyre ndi monga ESCOM United ndi Blantyre United.