Boma liyimitse kaye kusamutsa aphunzitsi otsogolera ziwonetselo – Kamlepo

Advertisement
Kamlepo Kalua

Kamlepo Kalua phungu wa dera la Rumphi East wafunsa mtsogoleri wa zokambirana mnyumba ya malamulo yemwenso ndi nduna ya maboma aang’ono, Richard Chimwendo Banda kuti ataganizira kuthandizirapo kuyimitsa kusamutsidwa kwa ogwira ntchito m’boma omwe ankatsogolera ziwonetselo za bata zofuna kukakamiza boma kuti liwakwezerebe ndalama za malipilo.

Ziwonetselo zi zinachitika masiku apitawo mu mzinda wa Lilongwe ndipo a Kalua ati boma likuyenera kuti limve madando a anthu ogwira ntchito m’bomawa ponena kuti anachita zomwe zili m’malamulo a dziko lino.

Chimwendo-banda
Chimwendo-banda: Zili mndondomeko ya boma.

Koma poyankhapo a Chimwendo Banda ati a Kalua sanapeleke mayina a aphunzitsi omwe akusunthidwa ku malo awo ogwira ntchito ponena kuti boma limasuntha ogwira ntchito kawirikawiri.

Mtsogoleri wa mbali yotsutsa a George Chaponda ati panakula mutu ndi poti atangomaliza kuchita ziwonetselo boma lidatulutsa zikalata zowasamutsa ku malo awo ogwira ntchito nthawi yomweyo, ndipo ati kumeneko ndi kuwawopseza ogwira ntchito m’boma.

A Shadreck Namalomba anayima kuti ayambe kuwelenga mayina a anthu omwe asamutsidwawa koma anakanizidwa kutelo ponena kuti funso silidabwere ndi iwo ndipo akuyenera kupeleka mayina akhale a Kalua omwe ndi eni funso.

Posachedwapa boma lidasamutsa aphunzitsi 13 omwe ambiri mwa iwo ndi omwe ankatsogolera ziwonetselo zopempha boma kuwawonjezera malipilo awo ndi 44%.

Zikalata zowasamutsa zomwe Malawi24 inawona zinatsindika kuti aphunzitsiwa akuyenera kukapezeka ku malo awo a ntchito komwe awasamutsilaku pompopompo, nkhani yomwe yawutsa kukokana pakati pa aphunzitsi ndi unduna wa zamaphunziro.

Mabungwe osiyanasiyana atsilirapo mulomo kuti kusamutsidwa kwa aphunzitsiwa ndi ndale.